Nkhani

Theng’eneng’e pakukwera kwa mtengo wa mafuta

Listen to this article

Theng’eneng’e labuka pakati pa boma, a mabizinesi komanso Amalawi chifukwa cha kukwera kwa mtengo wa mafuta a galimoto komanso anyale sabata yathayi ndipo aliyense mwa maguluwa akufuna kukokera mbedza kwake.

Nthambi yoyang’anira za mafuta ya Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) italengeza za kukwera mtengo wa mafutawo Loweruka sabata yatha, a mabizinesi monga oyendetsa galimoto zonyamula anthu adakangalika kuyamba kuchuna mitengo.

Aminibasi ena akweza kale mitengo

Izi amachita polingalira kuti monga mwachitsanzo, oyendetsa maminibasi amati boma lidawachepetsera chiwerengero cha anthu omwe anganyamule paulendo kutanthauza kuti ndalama yomwe amapeza pa ulendo umodzi idatsika.

“Taganizani, basi ya anthu 14 inyamule anthu 10 ndipo alipire K700 aliyense ndiye kuti ukupanga K7 000. Pomwepo ugulepo malita 5 a mafuta pa K1 150 ndiye kuti waononga K5 750 n’kutsala ndi K1 250 ndiye ukupanga bizinesi kapena ukungothandiza anthu basi?” adatero a Joakim Kaunda mmodzi mwa oyendetsa maminibasi ku Lilongwe.

Awo akudandaula chotero, ena akuti zonse zikuchitikazi pamtherankhani pake ndi iwowo ndipo ali ndi nkhawa kuti a maminibasiwo ndi amalonda ena akakakamira kukweza mitengo ndiye kuti moyo uwawa kwambiri chifukwa ndalama nayo ikuvuta.

“Kungoti poti zonse tikuzimvera m’malipoti osiyanasiyana koma pempho ndi loti omwe akukhudzidwa ndi kukonza mitengowo aganizire kuti Amalawi akhala bwanji, kodi munthu wovutika kumudzi agwira mtengo wanji?” adatero a Amon Chagunda a ku Lilongwe.

Koma pofuna kuziziritsa mitima ya Amalawi, boma kudzera kumaunduna a zamalonda komanso unduna wa zamtengatenga lachenjeza a mabizinesi onse kuti pasapezeke wofuna kutengerapo danga kuti adyere masuku pamutu Amalawi.

Ilo lati likhala likuunika momwe malonda akuyendera makamaka pankhani ya mitengo ndipo lati yemwe apezeke atakweza mitengo zakezake akhaulitsidwa ndi boma.

M’kalata yomwe maunduna awiriwo adatulutsa kukwera kwa mtengo wa mafuta kutangolengezedwa, idanenetsanso kuti onse abizinesi zonyamula anthu monga amaminibasi asamale pankhani ya mitengo yonyamulira anthu.

Chikalatacho chidati: “Mitengo yamafuta siyili bwino padziko lonse lapansi komanso kupatula apo, ndalama ya Kwacha idagwa mphamvu poyerekeza ndi ndalama zikuluzikulu.”

Bungwe la eni maminibasi la Minibus Owners Association of Malawi (Moam) nalo lidatulutsa kalata yake kutsutsa malipoti omwe anthu amafalitsa kuti lakweza mitengo yonyamulira anthu.

“Tikafuna kulengeza chilichonse timagwiritsa ntchito kalata yomwe imakhala ndi chizindikiro chathu. Ngati palibe chizindikiro chathu ndiye kuti uthenga umenewo ndiwabodza. Pakali pano sitidakwenze mitengo yonyamulira anthu,” idatero kalatayo yosainidwa ndi mlembi wake a Coxley Kamange.

Koma mkulu wa bungwe la anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito katundu la Consumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito adati ngakhale kudali kosatheka kuti mtengo wa mafuta usakwere, bungwe la Mera likadalingalira zokwenza mafutawo pang’onopang’ono.

“N’zoona mtengo wa mafuta umayenera kukwera kumene koma akadalingalira kukwenza pang’onopang’ono osangoti kamodzi n’kamodzi chifukwa kutero anthu amamva ululu waukulu kwambiri,” adatero a Kapito.

Kadaulo pa zachuma Milward Tobias adati boma la Malawi lilibe mphamvu iliyonse pa malonda a mafuta makamaka pa nkhani za mitengo kupatula kungoonetsetsa kuti mafutawo akupezeka.

Mkulu wa bungwe la Mera a Henry Kachaje adalengeza Loweruka sabata yatha kuti kuyambira Lamulungu lapitali, mtengo wa mafuta udakwera motere; Petulo uli pa K1 150 kuchoka pa K899.20, Diziro ali pa K1 220 ndipo mafuta a nyale ali pa K833.20 kuchoka pa K719.60.

Maiko oyandikana nafe monga South Africa, Botswana, Zambia, Zimbabwe ndi maiko enanso nawo adakweza mtengo wa mafutawa potsatira kukwera mtengo pa dziko lonse lapansi.

Related Articles

Back to top button
Translate »