Nkhani

Tidacheza nawo bwanji?

Listen to this article

M’chaka cha 2015 tamva zikhulupiriro, miyambo komanso mbiri zosiyanasiyana za maderanso osiyana. Lero BOBBY KABANGO akutibweretsera macheza ochepa amene nkhani yake idatekesa anthu.

Afisi ogulitsa ku Dedza

Nkhani iyi idadzidzimutsa anthu ambiri kumva kuti pali bambo wina amene akugulitsa afisi. Iye adati fisi wamkazi ndiye amadula pamtengo wa K9 000 ati chifukwa akakuswera pamene wamphongo amapanga K8 000.bobby_kucheza

Mkuluyu ndi Njale Biweyo wa m’mudzi mwa Masakaniza kwa T/A Kaphuka m’boma la Dedza.

Biweyo adati ntchito ya afisiwo ndi kuteteza usiku, kusakira nyama komanso kukwera ngati muli paulendo. Adati fisi ndi ndege yapansi yomwe imathamanga kwambiri.

Pamene timacheza naye, mkuluyu n’kuti ali ndi afisi awiri koma adati ena adawagulitsanso chifukwa adali nawo asanu.

Iye adati adayamba mu 1965 kuweta afisi. Iye ntchito yake akuti ndi ya ulonda ndipo kudzera m’tchitoyi, adapeza nawo afisiwa amene amamuthandiza pantchito yake. Komwe kukukhala mkuluyu adatilozera ampingo wina womwenso ukutetezeka ndi fisi wamkazi.

 

Dzina la Kachindamoto lidabwera bwanji?

Chaka chimenechi tidacheza ndi Senior Chief Kachindamoto wa m’boma la Dedza amene adatifotokozera momwe dzina lake lidabwerera.

Mfumuyi idati Chidyaonga ankamenya nkhondo kwambiri ndipo sankaopa. Azungu amene ankamenya nawo nkhondoyo adagonja ndi Chidyaonga. Anthu poona momwe mkuluyu akumenyera nkhondo adangomutcha dzina la Chidyaonga.

Mfuti kuti itulutse chipolpolo mukaomba n’chifukwa cha wonga umene ukayaka umaphulika kuti phuu! Ndiye chifukwa ankalimbana ndi zimenezi, anthu adangoti Chidyaonga, kutanthauza kuti akumadya wonga wa mfuti.

Kachindamoto nayenso sankaopa nkhondo. Iyeyu sankaopa ngakhale zitavuta maka ngakhalenso moto umene amapanga nawo mwakutimwakuti monga mukumvera dzinalo.

 

Wotentha thupi sayandikira ng’ombe

Mkazi amene thupi lake ndi la moto akuti sayenera kuyandikira ng’ombe kapena khola lake kuopetsa kuzibalalitsa chifukwa thupi lake ndi la moto. Izi ndimalinga ndi zikhulupiriro za Angoni ena achigawo chapakati koma kumva kwa ena kuchigawo cha kumpoto kwa dziko lino akuti mkazi sayandikira ng’ombe kuopetsa kuti asulutsa zizimba pakholalo.

Tidacheza ndi nyakwawa Chimpeni ya kwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu. Iye adati thupi la mayi amene adathera msinkhu ndipo wayamba kukhala kumwezi limakhala loopsa ku ng’ombe.

Iye adati mayi ameneyu saloledwa kuti adutse pakati pa ng’ombe zija zikamayenda kapena zikamawetedwa. Salolanso kuti alowe m’khola lake. Sangazikuse, sangakame kapena kutsekera pakhomo. Sangalowe m’khola ngakhale kukachotsa ndowe.

Nyakwawayi idati imakhulupirira kuti ng’ombezo zimabalalika ndipo zimayamba kugona m’thengo.

 

Kusakatula malongedwe a ufumu wa Chitumbuka

Apa tidacheza ndi nyakwawa Chibochaphere, ku Nkhamanga Kingdom m’boma la Rumphi atangolongedwa ufumu.

Iye adati polonga ufumu wa Chitumbuka, pamakhala timiyambo tina tomwe wolongedwa ufumu ayenera kutsata. Choyamba, dzina likadziwika la amene alowe ufumu, dzinalo limayenera lipite kwa Sawira Chikulamayembe kuti akalivomereze. Monga mwamwambo, kwa Sawira supita chimanjamanja koma kukwapatira kangachepe m’manja. Kumeneko timati ‘kuluvya’ pa Chitumbuka.

Polonga ufumu pamakhala madyerero kotero pamakonzeka magule, zakudya zambiri kuphatikizapo mowa ndi thobwa kuti anthu adzasangalale. Komanso monga mwamwambo kwa Sawira osalephera kupititsa ng’ombe yamchira kuti nawo akatsuke mkamwa.n

 

Related Articles

Back to top button