Chichewa

‘Tidakhulupirirana tsiku loyamba’

Listen to this article

 

Chikondi chidayambira kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College komwe Dennis Lupenga akuti atakumana ndi Sheila Chimphamba m’chaka cha 2013 pomwe onse amachita maphunziro, adakhulupirirana tsiku lomwelo.

Awiriwa adamaliza maphunziro awo ndipo Sheila amagwira ntchito muofesi ya mapolojekiti komanso ndi mkonzi wa mapologalamu kuwayilesi ya Zodiak pomwe Dennis ali ndi kampani yake ya zamakina a Internet.

Dennis akuti ubale wa awiriwa udayamba pa 9 April chaka chokumanacho

Awiriwa tsopano ndi thupi limodzi
Awiriwa tsopano ndi thupi limodzi

cha 2013 iye atauza njoyelo mwachindunji kuti akufuna kumukwatira

osati za chibwenzi monga momwe anthu ambiri amayambira.

“Ndidalibe nthawi yotaya nkumati ndili pachibwenzi chifukwa Sheila adandigwiriratu mtima ndipo ndidalibeso nthawi yoti ndimuone kaye ayi,” adatero Dennis.

Iwo akuti ngakhale uku kudali kusukulu, m’maganizo mwawo mudalibe za chibwenzi koma kuti akungoyembekezera tsiku lodzalowa m’banja ndipo panthawi yonseyi sadasiye makolo ndi abale awo mum’dima pozindikira kuti ubale wawo sudali wachibwana.

“Titakambirana, tidadziwitsa abale ndi makolo kuti azidziwa chifukwa timazindikira kuti pokangopita nthawi pang’ono tiwafuna kuti atimangire chinkhoswe ndi kutigwira dzanja pomwe tikukalowa m’banja,” adatero Dennis.

Iye akuti adakhala choncho mpaka chaka cha 2014 pa 9 August pomwe adamanga chinkhoswe nkuyamba kukonzekera ukwati omwe udachitika pa 2 April ku tchalitchi cha Katolika cha Maula ndipo madyerero adali ku Peak Gardens mumzinda wa Lilongwe.

“Sheila ndi mkazi wanzeru, wokongola, wachilungamo, wodzisamala ndi woopa Mulungu. Adandiwonetsa chikondi chenicheni monga momwe makolo anga adandionetsera,” adatero Dennis.

“Dennis ndi mwamuna wolimbikira, wodzichepetsa ndi wachikondi komanso wachilungamo.

Amandilimbikitsa ndikakhala ndi chofooka ndipo amandiphunzitsa kuthana ndi zokhoma,” adatero Sheila.

Dennis amachokera m’mudzi mwa Misale, Inkosi Mlonyeni m’boma la

Mchinji, pomwe Sheila amachokera m’mudzi mwa Chingala, T/A Masula m’boma la Lilongwe.n

Related Articles

Back to top button