Chichewa

Tidakumana Bwanji: ‘Padali pagalaja ku Area 25’

Garage ndi malo okonzera galimoto, koma ukachita mphumi malowa uthanso kudya nawo bwino monga momwe Mike Tembo adachitira.

Iyetu adasodzerapo msoti womwe akumanga nawo banja pa 7 May pa Sana Multi-Purpose Hall mumzinda wa Lilongwe.

Mike Tembo amagwira ntchito ku Leyland Motors koma amadziwika kwambiri chifukwa cha udindo womwe adali nawo kutimu ya Silver Strikers komwe ankagwira ngati mlembi. Njole yomwe mkuluyu watola ndi Annie Nkhandwe yomwe ikugwira ntchito ku JTI.

 Annie ndi Mike patsiku la send-off
Annie ndi Mike patsiku la send-off

Mike akuti mudali mu December 2013 pamene Mulungu adayamba kulumikizitsa awiriwa. Iye akuti adapita kugalaja ya ku Area 25 komwe amakakonzetsa galimoto. Amadikira kuti mpaka aikonze.

Akutitu mpaka cha m’ma 6 koloko madzulo ali pomwepo, anthu atayamba kuweruka ndipo apa naye Annie ataweruka amadutsira mbali yomwe kudali Mike. Apa nkuti awiriwa asakudziwana.

Koma likalemba lalemba basi, Mike adanunkhiza mafungo ndipo adamulonda mtsikanayo ngakhale samamudziwa. Moni ndi amene adali woyamba ndipo adasiyana atangofunsana maina.

Mosachedwa galimotoyo akuti adamaliza kukonza koma Annie n’kuti atanyamuka kale.

“Sindidachedwe, koma kukailiza kuyamba kumulonda mpaka ndidamuona akulowa pageti yakwawo. Ndidamukuwira, iyeamvekere, ‘you were following me?’

“Apo ndidalankhula molimba mtima ndimvekere, ‘ndimafuna ndidzaone pamene my future wife akukhala’ ndipo adaseka, ine ulendo,” adamusereula motero.

Kuchoka apa, awiriwa akuti amakumanabe, koma Mike akuti adapanga kaulendo kokaonera mpira wa Zambia pa Taytaz mmbali mwa msewu wa Mchinji osadziwa kuti mkuluyu alindi zina zoti achite kupatula mpirawo.

Chichewa chidagwa, namwali adayesera kuzemba koma Mike sadasinthe mawu. Njoleyi akuti idangomuuza kuti “ukhale kaye serious”. Mike adaonetsa izi ndipo ubwenzi udayamba.

Awiriwa apanga kale send-off sabata yatha pamene akukonzekera ukwati.

Mike amachokera m’mudzi mwa Kamuthuleni Tembo kwa Inkosi Mtwalo m’boma la Mzimba pomwe Annie ndi wa m’mudzi mwa Kamunthambani Nkhandwe kwa Mtwalo komweko ndipo onse akuchokera kumabanja achifumu.

 

Related Articles

Back to top button