Chichewa

Tidakumana ku BICC

Listen to this article

Themba William Mwale  adamuona koyamba  Grace Kadzakumanja  kumalo a zochitikachitika a Bingu International Convention Centre (BICC) komwe onse ankakatola nkhani.

Kadzakumanja adapita kumalowa ngati wokajambula zithunzi za kanema wa Channel for All Nations (CfAN) komwe amagwira ntchito, pamene Mwale adapita ngati mtolankhani kuchokera kunyumba youlutsa mawu ya Voice of Livingstonia, ofesi yawo ya ku Lilongwe.

“Ngakhale sitinayankhulane, chithunzithunzi chake chidakhazikika m’malingaliro anga, ndipo ndidamva kuchokera pansi pamtima wanga kuti uyu ndiye wanga wolonjezedwa uja,” adatero Mwale.

Ngakhale awiriwo amakhala mumzinda umodzi wa Lilongwe, zidatenga pafupifupi miyezi iwiri kuti aonanenso. Adaonananso kuhotelo ya Crossroads kogwira ntchito.

Mwale ndi Kadzakumanja lero ndi banja

Panthawi ya chisankho chapatatu cha 2019, Mwale adali ndi atolankhani anzake amuna pamalo ena oponyera voti mumzinda wa Lilongwe pomwe anyamatawa ankalankhula zambiri zotama Kadzakumanja m’maonekedwe angakhalenso khalidwe.

“Apa mpomwe ndinazindikira kuti ndikapitiriza kuchita chidodo, ndidzalilira ku utsi. Apa mpomwe ndinapanga chisankho choti ndiyambe kufunafuna nambala yake kwa anzake ogwira naye ntchito,” iye adatero.

Mwamwayi mmodzi wa ogwira  ntchito ndi Kadzakumanja yemwenso adali mnzake wa Mwale, adamukomera mtima ndikumupatsa nambalayo.

 Apa mpomwe adayamba kucheza momasuka, mpaka kufunsirana ndipo awiriwo anakwatirana pa 3 October 2020 ku Mzimba CCAP pomwe madyelero ake adali ku Mame Motel ku Mzimbako.

Pakadalipano, Mwale ndi  mkulu wa wailesi ya Voice of Livingstonia (VoL) pamene Kadzakumanja ndi mtolankhani ku CfAN, koma akupitiriza kaye maphunziro ake a ukachenjede pa sukulu ya Mzuzu University komwe akupanga maphunziro a Communication Studies.

Mwale amachokera m’mudzi mwa Chibisa kwa Jenda, Mfumu Mabilabo m’boma la Mzimba ndipo Kadzakumanja amachokera m’mudzi mwa Njolomole, Mfumu Njolomole m’boma la Ntcheu.

Related Articles

Back to top button
Translate »