Chichewa

‘Tidangoonana koyamba basi’

 

Kukumana kudziko la eni n’kudziwana kuti mumachokera kumodzi ndi chinthu chonyaditsa kwambiri moti kwa anthu ena chinansi chimayambira pomwepo ngakhale atakhala kuti amachokera m’zigawo zosiyana kwawoko.

Nkhani yathu lero ndi ya Wonder Msiska, wochokera m’boma la Karonga yemwe akugwira ntchito kuwayilesi ya Star—yomwe idaphathikana ndi kanema ya Timveni—yemwe pano ali pabanja ndi Hazel Silekile, naye wa ku Karonga, ndipo akugwira ntchito kukampani ya BETAMS Ltd.

Sadzalekana: Wonder ndi Hazel kutsimikiza kuti ali thupi limodzi
Sadzalekana: Wonder ndi Hazel kutsimikiza kuti ali thupi limodzi

Awiriwa adakumana ku Britain m’chaka cha 2008 komwe onse adapitira maphunziro ndipo adakaphana maso kumwambo wa chinkhoswe cha Mmalawi wina wake n’kukondana pomwepo.

“Zidangochitika kuti takondana basi. Ndikhulupirira ndi momwe Mulungu adakonzera. Choyamba, tonse tidapitira maphunziro kenako n’kuganiza zopita kumwambo wa chinkhoswe komwe tidakakumana,” adatero Wonder.

Iye adati atakumana kuchinkhosweko sipadatenge nthawi kuti ubwenzi uyambe mpaka kugwirizana za banja komweko.

Kusiyana ndi ena omwe amadikira tchuthi kuti akapange chinkhoswe kwawo, Wonder ndi Hazel akuti chinkhoswe chawo chidachitikira ku Mangalande komweko ku Sutton Coldfied m’chaka cha 2009.

“Si kuti udali mwano kapena kudzitama, ayi, koma tinkafuna kuti timaliziretu zomwe tidapitira kumeneko komanso panthawi yomweyo tionetse kuti tidakondanadi. Titabwerera kumudzi ku Malawi mpomwe tidayamba za mwambo waukulu wa ukwati,” adatero Wonder.

Ukwati wa awiriwa udachitikira mumzinda wa Blantyre m’chaka cha 2012 atabwerako ku Mangalande ndipo pano ali ndi mphatso ya ana aakazi awiri.

Wonder adanenetsa kuti atakhalanso ndi mwayi wina wosankha wachikondi akhoza kubwereza chisankho chake chifukwa iye mtima wake udakhazikika pa Hazel ndipo ndi khumbo lake kudzasungana naye mpakana kalekale.

Hazel adati kwa iye Wonder ndiye mbali imodzi ya thupi lake ndipo sangagwedezeke ndi chilichonse chifukwa mwa iye adapeza mwamuna wachikondi ndi wachilungamo.

Akuti iye akakhala, kaya n’kutchito, pakhomo ngakhalenso kunyumba saona chomulekanitsa ndi mwamuna wakeyu ndipo naye ali ndi chiyembekezo cha banja lapamwamba ndi lotsogola komanso latsogolo lowala.

Related Articles

Back to top button