Chichewa

‘Tidasala masiku 52 kuti Mulungu atiunikire’

Nthawi zambiri, anthu timatenga banja ngati sitepe pamoyo wathu basi koma tikalingalira momwe banja la m’busa komanso mlembi wa mkulu wa mpingo wa CCAP Reverend Vasco Kachipapa Banda ndi mkazi wake Madalitso Nyoli, mibadwo yobwerayi idzazindikira momwe banja la umulungu limakhalira.

Awiriwa akuti adakumana mu 1992 onse atasankhidwa kupita kusukulu ya sekondale ya Mitundu ndipo chikondi chawo chidayamba mu 1994 koma uku sikudali kuyamba kwa banja poti zambiri zidadutsapo.

Rev. Kachipapa adati mizati itatu ndiyo idagwira ntchito kuti awiriwa atseguke mmaso kutidi adalengedwa kudzakhala limodzi ndi kutumikira Chauta ngati bambo ndi mayi komanso odyetsa ndikusamala nkhosa zake.

Kachipapa ndi Madalitso: Lero ndi banja

“Mzati woyamba, ineyo ndidadwala tikadali kusukulu mpaka ndidapita kunyumba. Nditapeza bwino nkubwerako, Madalitso adabwera kudzandizonda ndipo aka sikadali komaliza. Pamenepa ndidazindikira kuti ndi umunthu weniweni,” adatero Kachipapa.

Iye adati chikondichi sichidasanduke mapeto azonse ayi koma chiyambi cha kudzifunsa ndi kupempha utsogoleri wa Mulungu.

“Mchaka cha 1997, tonse awiri tidayamba mapemphero ndi kusala kwa masiku 52 (Loweruka lokhalokha) kupempha Mulungu kuti atiunikire ngatidi tidali oyenera kukwatirana. Ndi mzati wachiwiri ndipo mzati wachitatu udali nthawi yomwe ine ndimapanga maphunziro a zaubusa ku Zomba, mkazi wanga adali atayamba kale ntchito ndipo adandithandiza kupereka malowolo ake omwe,” adatero Kachipapa.

Iye adati Chauta atavomereza zonse, ndondomeko zoyenera zidatsatidwa kufikira nthawi ya chinkhoswe m’chaka cha 1998 ndipo kenako ukwati woyera ku Ntchisi CCAP.

“Ndimakonda mkazi wanga kwambiri chifukwa cha mtima wake wabwino, amakonda kupemphera kwambiri ndipo simkazi wanga chabe koma mzanga muuzimu,” adatero Kachipapa.

Nawo mayi a kunyumba akuti (Madalitso) akuti abusawa ndi bambo wabwino wokonda banja lawo ndi wodziwa kusamala.

“Ndi bambo abwino kwambiri odziwa udindo wawo ndiokonda banja lawo komanso kusamala ana awo. Timapemphera limodzi, kuyenda limodzi, kudya limodzi mwachidule timapangira zinthu limodzi,” adatero mayiwo.

Kachipapa amachokera m’mudzi wa Makwenda mfumu yaikulu Chiseka ndipo Madalitso amachokera m’mudzi wa Khanda T/A Kalolo onse m’boma la Lilongwe. n

Related Articles

Back to top button