Chichewa

Tigwirane manja pothana ndi chisaka cha Nthochi

Listen to this article

Mkulu woona za mbewu za m’gulu la zipatso ku dipatimenti ya za kafukufukuku mu unduna wa zamalimidwe Felix Chipojola akuti nkhondo yolimbana ndi matenda a chisaka cha nthochi m’dziko muno siingaphule kanthu pokhapoka anthu atagwirana manja.

Iye adafotokoza kuti njira yokhayo yothana ndi chisaka ndikuchotsa nthochi zonse zakale ndikubzala zina.

Kukakamira nthochi zakale kukuchititsa kuti chisaka chizipitirira

Chipojola adati m’zomvetsa chisoni kuti alimi ena sakufuna kudzula nthochi zawo zakale zomwe zikuchititsa kuti matendawa asathe msanga m’dziko muno.

“Tidakagwirana manja ndikuonetsetsa kuti nthochi zonse zakale zachotsedwa,  matendawa akadatha ndipo m’dziko muno bwenzi mukupezeka ntchochi zochuluka,” iye adatero.

Malingana ndi mkuluyu, ngakhale alimi omwe adachotsa nthochi zakale ndikubzala zopanda matenda ali pachiopsezo cha matendawa chifukwa amzawo sakufuna kudzula nthochi zawo zakale zomwe zikhoza kuchititsa za tsopanozo kuti ziyambenso kugwidwa ndi matendawa.

Chipojola adati  matenda a chisaka cha ntchochi amafala ndi nsabwe zomwe zimatha  kuulukira m’minda ina.

“Ena akumaputsitsika akaona  nthochi zawo zikuoneka za thanzi koma akuyenera kudziwa kuti matendawa amabisala ndipo tsiku lina amadzavumbuluka,” iye adatero.

Woona za ulimi wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe  Harold Katondo adati adayendera m’maboma momwe mumalimidwa kwambiri nthochi m’dziko muno ndicholinga chofuna kupeza zomwe zikuchititsa kuti alimi azikakamirabe mbewu zakale.

“Pocheza nawo alimiwa amafotokoza kuti mbewu zawo zakale n’zokoma kwambiri komanso amatha kuzigwiritsa ntchito kuphikira zinthu zosiyanasiyana.

“Chodabwitsa n’choti ngakhale amayankhula zoterezi, sadayetserepo kulima kapena kudya nthochi zatsopanozi,” iye adatero.

Katondo adati izi zachititsa kuti ayambe kutolera mbewu zakalezi m’madera osiyanasiyana a m’dziko muno ndikuzikonza kuti zikhale zopanda matenda.

Iye adati akazikonza ndikuzichulukitsa adzazibwezera kwa alimi kuti azidzabzala.

Mkulu wa za ulimi m’boma la Thyolo Jackson Mkombezi adati alangizi m’bomali adayesetsa kuwafotokozera alimi za njirayi koma ntchito ya kalavula gaga yomwe  imakhalapo pochotsa ntchochi ndiyomwe ikuchititsa kuti mbewu zakale zizipezekabe.

“ Ntchitoyi ikadakhala yosavuta  ikadayenda mwachangu ndipo nthochi zambiri zikadachotsedwa ndikubzalidwa zina zopanda matenda,” iye adatero.

Mkuluyu adati  alimi omwe adabzala mbewu zopanda matenda mu 2015 pano akutsimba lokoma ndipo ambiri akupeza zokolola zamnanu.

 Mulanje ndi limodzi mwa maboma omwe ulimiwu umachitika kwambiri moti mkulu wa za ulimi m’bomalo Evelyn Chima akuti kuchepa kwa mbewu ndi ena mwa mavuto omwe amachititsa kuti azikakamirabe mbewu zakale.

“Poyambirira tidalandira mbewu yochepa moti alimi omwe adavomereza kubzala mbewu zopanda matenda sadalandire onse.

“Chaka chino  talandira mbewu yochuluka komanso alimi ena tawaphunzitsa kuti azitha kuchulukitsa ndikumagaira anzawo.

“ izi zithandizira kuti anthu ochuluka apeze mbewu,” iye adatero.

Chima adati alangizi a m’bomali akuyesetsa kugwira ntchitoyi ndi atsogoleri a mipingo, mabungwe komanso zipani ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo ulimiwu.

Related Articles

Back to top button
Translate »