Chichewa

Tikuchita bwanji ndi matewera?

Listen to this article

 

Thewera  loti  lagwiritsidwa ntchito limaipa mmaso komanso kudetsa kukhosi.

Mwina likakhala la mwana wako, komabe  ambiri limativuta kuyang’ana, kuligwira kapena kuchapa kumene.

Utchisi wathewera la nsalu  umaonekera komanso kusautsa anthu pakhomo.

Amayi ena opanda dongosolo amatha kusunga matewera ogwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali zomwe zimasokoneza pakhomo.

Mmaganizo awo amayi oterewa amati chimbudzi cha mwana nchosachititsa nyansi chasiyana ndi munthu wamkulu.

Koma izi sizoona. Chimbudzi ndi chimbudzi basi. Sichikondweretsa kuchiona.

Kuphatikiza apo, kulephera kusamala chimbudzi choti mwina muli matenda kungapangitse kuti matendawo afale mosavuta.

Tsopano kubwera kwa matewera a pulasitiki,  aja timangotaya tikagwiritsa ntchito, kwadzanso ndi utchisi wake omwe umakhudza anthu ochuluka m’madera omwe tikukhala.

Basitu, amayi ena omwe amagwiritsa ntchito matewerawa amangotayapo mwachisawawa nkumapatsa agalu zochita.

Mukudziwa inu khalidwe la galu. Kungotayapo matewerawa poyerayera kumapangitsa agalu kuti akoke izi nkumakasiya m’makomo mwa anthu ena kapena m’misewu kumene.

Koma aliponso amayi ena omwe sadikira galu kuti achiteizi. Ngati alibe dzala kapena malo ena osunga zinyalala, amangoponyapo matewerawa pali ponse bola zachoka pakhomo lawo.

Kukhala kotereku nkosokoneza. Thewera la mwana wako lisapsinje anthu okuzungulira.

Pamene tikukhala m’maderamu timayenera kuonetsetsa kuti zochita zanthu zisasokoneze moyo wa anzathu.

Iwe  usamapeze mtendere pochita chinthu chomwe chichotse mtendere wa wina.

Tisanagwiritse ntchito thewera la pulasitiki tiganizire kuti tilisamala bwanji kuti lithere pakhomo pathupo, lisakafike pakhomo pa mnzathu kapenanso kuonedwa ndi ena omwe sizikuwakhudza.

M’madera tikukhalamu tatopa ndi mchitidwe womangotaya matewera paliponse.

Chonde Amayi uvewu tisiye. n

Related Articles

Back to top button