Nkhani

Tikulumirabe ana chakudya?

Listen to this article

Masiku ano pomwe matenda a Edzi afala mwa nkhani nkhani pakufunika kuonetsetsa komanso kusintha zinthu zina zomwe anthu timachita makamaka mokhudzana ndi ana.

Mwachitsanzo, anthu tili ndi chizolowezi chosendera nzimbe ana. Akakhala ana oti mano akungoyamba kumera, tikasenda nzimbe inja timailumalumanso kuti isamuvute kutafuna. Kuonjezera apo, timakondanso kuwalumira ana chakudya china ngati mango, magwafa ndi zina zotero.

Izi sitimangochitira ana athu komanso a abale, anzathu ndi enanso oti tangokumana nawo. Zikuchitika izi tsiku ndi tsiku.

Koma tikamachita izi ambiri sitilingalirapo kuti kodi mthupi mwathu muli bwanji pa nkhani ya matenda omwe tingathe kufalitsa kwa anawa kudzera mumate komanso magazi omwe nthawi zina amatha kutsalira pa chakudya chomwe mwana wapatsidwa.

Ambiri timangoti bola tamuthandiza mwana olilira chakudyayo.

Ngakhale matenda a Edzi amafalikira kwambiri mnjira yogonana, nthawi zina anthu timayiwala kuti mkamwa mukhonzanso kudzera matendawa makamaka ngati anthu ogawana chakudyachi ali ndi zilonda mkwamwa.

Nzimbe ndi chimodzi mwa chakudya chomwe nthawi zina chimachekacheka mkamwa choncho nkosavuta kuti mabalawa atulutse magazi omwe akhonza kukumana ndi magazi a mkamwa mwa mwana ngati mwanayonso atadzicheka kapenanso ngati ali ndi bala nkamwa.

Pambali pa matenda a Edzi, palinso matenda ena ngati chiseyeye omwe munthu ungathe kumpatsira mwana kupyolera mchankudya chomwe wamulumira.

Anawa a msinkhu ogairidwa chakudya motere kapena kusenderedwa nzimbe sadziwa kuti kunja kuno kuli matenda amtunduwu. Sangadziwe kuopsa kwa matendawa kapena kuti angawapewe bwanji.

Choncho nkoyenera kuti ife amene tikudziwa za izi titengepo gawo lalikulu poteteza miyoyo ya anayi posaiika pachiopsezo chotenga kachirombo ka Edzi munjira zogairana chakudya poyesetsa kuti tigwiritse ntchito zida ngati mpeni mmalo mwa mano.

Ngakhale mauthenga ali ponseponse kuti tikayezetse magazi, si tonse tidayezetsa nkudziwa kuti tili ndi kachilombo kapena ayi.

Choncho ndi bwino kungokhala wanthumazi ndi osamalitsa makamaka poonetsetsa kuti moyo wa ana osazindikira zinthu ukutetezedwa ku nthenda zomwe zingathe kupeweka potsata njira zabwino zogawirana chakudya.

Related Articles

Back to top button