Chichewa

‘Timakakonza za ntchito’

Listen to this article

 

Wakaona nyanja adakaona ndi mvuwu zomwe. Mauwa apherezedwa ndi ukwati wa Amos Mazinga wa ku Dowa m’mudzi mwa Ngozi, T/A Chiwere, ndi Regina Mkonda wa m’mudzi mwa Reuben, m’boma la Mulanje.

Awiriwa akuti adakumana kuofesi ya aphunzitsi ku Nathenje m’chaka cha 2014 atamaliza maphunziro a zauphunzitsi, komwe akuti amakolongosola za malo omwe azikagwirira ntchito koma ulenje udabzola mlingo ataphana maso.

Amos adati iye atangoonana maso ndi maso  ndi Regina, mtima wake udadumpha kwambiri moti adalakalaka zotuluka muofesimo kuti akadzione ngati akukwanira kulankhula donayo.

Amos ndi Regina kupsopsonana patsiku  la ukwati wawo
Amos ndi Regina kupsopsonana patsiku
la ukwati wawo

“Zimene zidandichitikira sizidandichitikileponso m’moyo mwanga. Ine ndi mmodzi mwa anthu omasuka komanso opanda mantha ngakhale pamaso pa anthu, koma tsiku ili lokha ndidaona nyenyezi yothobwa m’maso,” adatero Amos.

Iye akuti panthawi yomwe iwo amayembekezera kuthandizidwa mpamene adapeza mwayi womulankhulira msungwanayo ndipo adacheza bwino kwambiri mpakana kupatsana nambala za foni za m’manja.

Kusiyana kwa pamenepo kudali madzulo atalandira thandizo, koma kudali kusiyana pamaso chabe chifukwa macheza awo adapitirira kudzera pafoni.

“Tidakhala nthawi yaitali tikuchezerana pafoni mpaka tsiku lina nditalimba mtima ndidayambitsa nkhani yachikondi, koma kunena zoona ndidalimbana naye mpakana adatheka moti lero ndikakhala ndimadziwa kuti nane mpatali,” adatero Amos.

Iye akuti chikondi chake pa Regina chidakula kwambiri kaamba ka khalidwe lake lokonda kupemphera, kuchita zinthu mwanzeru ndi modzilemekeza komanso mwansangala.

Regina adati iye poyamba adamutenga Amos ngati mchimwene koma pang’onopang’ono chikondi chidayamba kumugwira moti samafunanso kuti Amos adzagwe m’manja mwa munthu wina koma iye.

Iye adati ngakhale amakanakana poyamba mtima wake udali utalola kale koma amafuna kuona ngati Amos adalidi munthu wachilungamo, wosangofuna kumuseweretsa.

“Sindidafune munthu woti kugwa naye m’chikondi panthawi yochepa kenako nkukhumudwitsidwa, ndiye ndimayenera kuonetsetsa kuti ndikudzipereka m’manja mwa woyeneradi,” adatero Regina.

Iwo akuti zonse zitalongosoka adaganiza zokaonekera kumakolo kuti azidziwa ndipo makolo a mbali zonse adali okondwa ndi nkhaniyi mpaka adathandizapo kuti chinkhoswe chichitike mpakana ukwati woyera womwe adakadalitsira mumpingo wa CCAP. n

Related Articles

Back to top button
Translate »