Chichewa

‘Tinkaimba limodzi kwaya’

Listen to this article

 

Mdalitso suoneka pakudza munthu umangozindikira walandira mphatso koma osadziwa kuti yachoka kuti malingana ndi ntchito zomwe ukuchita monga momwe a mvula zakale adanenera kuti ntchito iliyonse ili ndi mphotho yake.

Kudzipereka komwe adachita Joseph Kaluwa ndi Victoria Mdala Kaluwa m’chaka cha 2014 posankha kutumikira Mulungu m’njira ya kwaya patchalitchi ya mpingo wa chikatolika wa Don Bosco ku Lilongwe kudawalunjikitsira kumoyo wina wopambana.

Awiriwa akuti amaimba kwaya limodzi ndipo kenako adagwa m’chikondi atakhutitsidwa kuti iwo adalengedwa kuti adzakhale limodzi ngakhale kuti adabadwira ndi kukulira mbali ziwiri zosiyana za dziko lino la Malawi.

Joseph ndi Victoria tsiku la ukwati wawo
Joseph ndi Victoria tsiku la ukwati wawo

“Ndinkasangalala tikamaimba ndipo ndikamamva mawu ake a nthetemya. China chomwe chidanditenga mtima nchakuti amakonda kupemphera ndi kutumikira kutchalitchi,” adatero Joseph.

Iye adati adayesetsa kuti awiriwa akhale pachinzake cha mchimwene ndi mlongo kwa miyezi yokwana 6 ndipo ataona kuti ena akhoza kungobwera nkuphumitsa adaganiza zomasuka ndipo mwa mphamvu ya Mulungu yomwe idawakumanitsa zinthu zidatheka.

Joseph adaonjeza kuti panthawiyo nkuti atangomaliza maphunziro ake a zowerengera ndalama koma asadayambe ntchito ndipo Victoria adali akadali pasukulu koma iwo sadawerenge izi pozindikira kuti Mulungu adzawatsogolera.

“Tidalimba mtima ndipo tidasangalala kuti makolo ndi abale athu adatithandiza kwambiri mpaka tidapanga chinkhoswe ngakhale kuti chidali cha m’nyumba koma pambuyo pake tidamanga ukwati woyera omwe tidakadalitsira ku Tchalitchi ya Don Bosco pa 29 September 2015,” adatero Joseph.

Victoria adati sadalabadire zoti panthawiyo Joseph samagwira ntchito iliyonse chifukwa iyeyo adakonda munthu osati chuma ndipo adali wokondwa kwambiri makolo ake atavomereza chibwenzicho.

Iye adati ali ndi loto limodzi lokhala pa banja la ulemu ndi lowopa Mulungu monga momwe zilili pano.n

“Pemphero langa ndilakuti zipitirire monga momwe zilili pano. Ndili pabanja lokoma kwambiri ndipo ndimakonda mwamuna wanga kwambiri ndi ana anga atatu,” adatero Victoria.

Joseph amachokera ku Nthalire mboma la Chitipa ndipo pano akugwira ntchito ku nthambi yolondoloza za momwe ndalama zikuyendera ya Financial Intelligence Unit ndipo Victoria amachokera kwa T/A Kwataine ku Ntcheu ndipo akugwira ntchito ku nthambi ya za nkhalango m’boma.

 

 

Related Articles

Back to top button
Translate »