Chichewa

‘Tinkakalongosola za ntchito’

Listen to this article

 

Okaona nyanja amakawonadi ndi mvuu zomwe. Mawuwa apherezedwa ndi ukwati wa Amos Mazinga wa ku Dowa m’mudzi mwa Ngozi T/A Chiwere ndi Regina Mkonda wa ku Mulanje mmudzi mwa Reuben.

Awiriwa akuti adakumana kuofesi ya maphunziro ku Nathenje mu 2014 atamaliza maphunziro a zauphunzitsi komwe amakolongosola za komwe azikagwirira ntchito.

Amos adati iye atangomuona Regina, mtima wake udadumpha kwambiri.

Amos ndi Rehina kupsopsonana tsiku la ukwati wawo
Amos ndi Rehina kupsopsonana tsiku la ukwati wawo

“Ndine mmodzi mwa anthu omasuka ngakhale pagulu koma tsikulo ndidaona nyenyezi yothobwa mmaso,” adatero Amos.

Iye akuti panthawi yomwe iwo amayembekezera kuthandizidwa, mpamene adapeza mwayi wolankhulana ndi msungwanayo ndipo adacheza bwino mpaka kupatsana nambala za foni.

Kusiyana kwa pamenepo kudali madzulo atalandira thandizo koma kudali kusiyana pamaso chabe chifukwa macheza awo adapitirira kudzera palamya.

“Tidakhala nthawi yaitali tikuchezerana palamya mpaka tsiku lina nditalimba mtima ndidayambitsa nkhani ya chikondi koma kunena zoona ndidalimbana naye mpaka adatheka,” adatero Amos.

Iye akuti chikondi chake pa Regina chidakula kwambiri kaamba ka khalidwe lake lokonda kupemphera, kuchita zinthu mwa nzeru ndi modzilemekeza komanso mwasangala.

Regina adati iye poyamba adamutenga Amos ngati mchimwene koma pang’onopang’ono chikondi chidayamba kumugwira moti samafunanso kuti Amos adzagwe m’manja mwa munthu wina koma iye.

Iye adati ngakhale amakanakana poyamba, mtima wake udali utalola kale koma amafuna kuona ngati Amos adalidi munthu wachilungamo wosangofuna kumuseweretsa.

“Sindidafune munthu woti kugwa naye m’chikondi panthawi yochepa kenako nkukhumudwitsidwa ndiye ndimayenera kuonetsetsa kuti ndikudzipereka m’manja oyeneradi,” adatero Regina.

Ukwati adamangitsa kumpingo wa CCAP.

 

Related Articles

Back to top button