Nkhani

Tionana 2019— Mafumu

Listen to this article

Mafumu achenjeza kuti aphungu omwe sakufuna kumva madandaulo awo pankhani ya lamulo lokhudza malo a makolo adzakumana ndi chipande pachisankho cha 2019.

Izi zidanendwa Lachitatu pomwe mafumu ochokera mbali zosiyanasiyana motsagana ndi womenyerera ufulu wa anthu pankhani malo m’maboma a Thyolo ndi Mulanje, Vincent Wandale, adakapereka chikalata cha madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo.

Mafumu kuchokera zigawo zonse  m’dziko muno patsiku la chionetsero
Mafumu kuchokera zigawo zonse m’dziko muno patsiku la chionetsero

Nkhani yomwe mafumuwa ikuwapweteka ndi yosintha lamulo lokhudza malo a makolo omwe iwo akuti amayenera kukhala pansi pa ulamuliro wawo pomwe lamulo latsopanoli likuti anthu azikhala ndi ulamuliro pamalo otere.

Lamuloli lidasinthidwa m’Nyumba ya Malamulo ndi kuvomerezedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika mwezi wa September chaka chino, koma mafumuwa akufuna kusinthaku kubwezedwe mpaka iwo adzafunsidwe maganizo awo pankhaniyi.

Gululi, lomwe lidakumana ndi mavuto kuti lipereke madandaulowo ku Nyumbayi, lidanyamula zikwangwani zochenjeza kuti aphungu omwe adasintha lamuloli adzawafuna mu 2019 chisankho chikafika.

Mafumu kuchokera zigawo zonse  m’dziko muno patsiku la chionetsero
Mafumu kuchokera zigawo zonse m’dziko muno patsiku la chionetsero

Zikwangwani zina zidati: “Akuluakulu a zamalo yeserani kubwera m’madera mwathu mudzaone chidameta nkhanga mpala” komanso, “A Pulezidenti ndi aphungu ikani maso anu pa 2019”.

Mudandaulo lawo m’chikalata chomwe adapereka kwa aphungu ndipo adalandira ndi mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma yemwenso ndi pulezidenti wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), Lazarus Chakwera,  mafumu adati malo a makolo ndi awo osiyiridwa ndi makolo.

Pothirirapo ndemanga, Wandale, yemwe akuyimirira anthu a ku Thyolo ndi Mulanje, adachenjeza boma kuti lisiye kupondereza anthu chifukwa cha malo awo omwe.

Atalandira chikalata cha madandaulocho, Chakwera adatsimikizira mafumu ndi gululo kuti madandaulo awo akafika m’Nyumba ya Malamulo kuti akaunikidwe.

Koma ndunda ya zamalo ndi chitukuko cha m’midzi, Atupele Muluzi, akutsindika kuti lamulo latsopanoli ndi lopindulira anthu akumudzi powapatsa mphamvu zolamulira malo omwe akugwiritsa ntchito.

“Lamulo lakale limatanthauza kuti malo a makolo ndi a gulu, choncho munthu sangamasuke kupanga nawo chitukuko chenicheni. Chomwe lamulo latsopanoli likubweretsa n’chakuti munthu azikhala ndi makalata osonyeza umwini moti akhoza kukatengera ngakhale ngongole ku banki ngati chikole chifukwa pali umboni kuti ndi malo ake,” adatero Muluzi.

Iye adati lamuloli likuperekanso mpata kwa achinyamata ndi amayi okhala ndi malo m’dzina lawo kutanthauza kuti amayi ndi ana amasiye azikhala otetezedwa kunkhanza zolandidwa malo.

Related Articles

Back to top button