Chichewa

Tisiyanitse kukongola ndi kuphweka

Listen to this article

Amayi ndi atsikana ambiri tikafunsiridwa ndi munthu wokwatira, timakwera mumtengo, kumva bwino kuti ngakhale uja ali ndi mkazi wake waponyabe maso pa ine ndiye kuti ine ndiliko bwino poyerekeza ndi mkazi wake.

Enanso omwe amachita zibwenzi ndi abambo okwatira maganizidwe ake amakhalanso otere: Umaona ngati kuti iwe wachibwenziwe ndiwe swopambanirako kusiyana ndi mkazi ali kunyumba.

Mayi wanga adandiuza, ndipo ndimakhulupilirabe mpaka lero, kuti kufunsiridwa ndi munthu wokwatira si chinthu chopambana koma chomvetsa chisoni.

Iwo adati bambo wa banja lake akati wakukonda, udzidabwe ndipo udandaule kuti waona chiyani pa iwe.

Ndi nkhani ina kuti wakunamiza kuti ngosakwatira, koma ukudziwa ndithu kuti ali ndi mkazi kunyumba, iye nkulimba mtima nkubwera kwa iwe ndi mawu achikondi ndiye kuti wakudelera; wakuona kuphweka.

Ambiri mwa abambowa amakukweza mumtengo pokuuza zabwino zako poyerekeza ndi mkazi wawo. Iwe ukakhala watulo umangogodoka.

Ena amakuuza za mavuto omwe akukumana nawo kunyumba, iwe nkumadziona ngati msamaliya woti uthandize kukonza moyo wa bambo yemwe sakusangala kunyumba kwake.

Koma zoona zake nzakuti abambo ambiriwa amangofuna kukuseweretsa. Amangofuna akupusitse ndiye iwe ukakhala opepera ndi wotengeka ndi timau tabodza tachikondi umagwa mmbuna.

Ena mwa abambowa amakuuza kuti ali ndi maganizo othetsa banja lawo. Iwe nkumalimba mtima uli ndikalowa ndine mnyumbamo mzangayo akathamangitsidwa.

Umangodabwa zaka zikupita ana nkumabadwa mnyumba muja bamboyo akuti sakukondwamo. Ndipo kawirikawiri likatha banjalo abambo oti amachita chibwenzi ndi iwe samakukwatiranso. Amakasaka wina mzimayi ‘wakhalidwe’ iwe nkungokugwiritsa fuwa la moto.

Nkutheka mwina wakukondadi bamboyo, koma bwanji ayambe wathana ndi mkazi wake asanabwere kwa iwe?

Osapusitsidwa kuti mwakongoletsa; ayi ndithu, mwangophweka.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »