Chichewa

Tsala bwino 2016

Listen to this article

 

Pamene tikutsendera chaka cha 2016, akadaulo ena pandale ati zochitika m’chakachi zikutsimikiza kuti Amalawi akuchenjera ndiye andale asamale mu 2017.

Akadanena izi kaamba ka mipungwepungwe imene idagwedeza zipani za ndale, kulephera kwa zipani zina pa zisankho zapadera zimene zidalipo komanso misamuko imene idagundika mu 2016.

Katswiri wa za ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Boniface Dulani, adati zochitika pa dale m’chakachi ndi chenjezo kwa andale kuti aunike bwino khalidwe lawo madzi asadafike m’khosi.

“Masiku ano anthu adachangamuka ndipo safuna kugwiritsidwa ntchito n’kutayidwa. Mikangano imene idabuka m’zipani komanso zotsatira za chisankho, muona kuti ngakhale andale samayembekezera kuti zingayende choncho,” adatero Dulani.

M’chakachi mudali chisankho chapadera

Iye adati kale Amalawi ankatsatira ndale zofumbatitsana koma adazindikira kuti ndale zotere zimangowaphwanyira ufulu osankha atsogoleri.

Mkulu wa Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adati nthawi yakwana yoti a ndale ayambe kudziyika m’gulu la ena onse osati kudzipatula.

Iye adaonjeza kuti mikangano ina m’zipani imayamba kaamba ka njala yofuna maudindo ndiye atsogoleri a zipani azigonjerana nkutsatira zomwe zamangidwa kumsonkhano waukulu wa zipani zawo.

Chipani cha MCP chidagwedezeka ndi mikangano mpaka akuluakulu ena adachotsedwa pomwe ena adaimikidwa. Mikanganoyo idayamba ndi apampando a makomiti a m’maboma omwe posakondwa ndi kusinthidwa kwa maudindo ena a mukomiti yaikulu, adatengera chipanichi kukhoti pofuna kukakamiza chipani kupangitsa msonkhano waukulu wosankha maudindo.

Chipanicho chidachotsa mmodzi mwa mizati yake, Felix Jumbe yemwe ndi phungu wapakati m’boma la Salima pamodzi ndi akuluakulu ena monga wapampando wa m’chigawo cha kummwera Chatinkha Chidzanja-Nkhoma ndi Azam Mwale. MCP idaimitsa akuluakulu Jessie Kabwira phungu wa ku Salima yemwe panthawiyo anali mneneri wachipani komanso mzati wina wa chipanicho Joseph Njobvuyalema.

Nako ku People’s Party (PP), kudali kusamvana kwa m’chipanicho kudayamba kaamba ka kubindikira kwa mtsogoleri wake Joyce Banda kumaiko akunja.

Kusowa kwa Banda kudabweretsa mikangano yolimbirana utsogoleri m’chipanichi ndipo pomwe iye adasankha phungu wa kumwera kwa boma la Salima Uladi Mussa kukhala wogwirizira utsogoleri wa chipanichi, akuluakulu ena sadagwirizane nazo.

Mmodzi mwa akuluakuluwo, Christopher Mzomera Ngwira yemwe ndi woyang’anira chipanichi m’chigawo cha kumpoto adati njira yomwe Banda amatsata poyendetsa chipanicho idali yosokonekera ndipo iye adati kudali bwino mtsogoleriyo akadatula pansi udindo wake kuti chipanichi chione njira zina.

Akuluakulu ena a chipanicho, kuphatikizapo yemwe adaima ndi Banda pachisankho, Sosten Gwnegwe komanso Brown Mpinganjira atuluke m’chipanicho.

Naye mneneri wa chipanicho Ken Msonda adatuluka PP mu September. Iye adakalowa DPP.

Nacho chipani cha United Democratic Front (UDF)  chidali ndi mikwingwirima potsatira ganizo logwira ntchito ndi chipani cholamula m’Nyumba ya Malamulo kapena ayi. Aphungu onse a UDF adakhamukira ku mbali ya boma kupatula phungu wakumpoto kwa boma la Balaka Lucius Banda. n

Related Articles

Back to top button
Translate »