Chichewa

Tsiku lokumbukira usodzi

Listen to this article

Chaka chino zangokumanizana ndendende kuti lero, pa 21 November, ndi tsiku loganizira nsomba ndi ntchito za usodzi padziko la pansi (World Fisheries Day). Bungwe la United Nations lidakhazikitsa tsikuli pokhudzidwa ndi kuchepa kwa nsomba komanso kusakazika kwa zachilengedwe zam’madzi padziko lonse.

Patsikuli, asodzi padziko lonse amakonza zochitika zosiyanasiyana zozindikiritsa anthu kufunika kwa nsomba pamiyoyo ndi chitukuko cha maiko awo, dziko lapansi komanso kusamalira zachilengedwe zammphepete mwa nyanja.

Kwathu kuno, tsikuli lidakumbukiridwa koyamba chaka chathachi pamwambo umene udachitikira m’boma la Nkhata Bay. Mwambowo udakonzedwa ndi bungwe la Ripple Africa.

Miyoyo ya anthu oposa 400 000 amene amadalira usodzi paumoyo wawo ili pa chiopsezo, kaamba kochepa kwa nsomba m’nyanja ndi m’mitsinje ya dziko lino. Chimene chikuchitika pakalipano n’chakuti pamene mitundu ya nsomba zofunika kwambiri monga chambo, kampango ndi utaka zikusowa, mpamene bonya akuchulukirachulukirabe.

Mtsogolo muno tidzafotokozera chifukwa chiyani zinthu zikubwerera chammbuyo chonchi, koma pakalipano n’kofunika kulimbikitsa njira zimene zikutsatidwa poteteza nsomba kuti anthu ambiri asadzasowe pogwira zisanatheretu.

Usakhale udindo wa boma lokha komanso mafumu, asodzi eni ake, anthu wamba, mabungwe monga a Ripple Africa, USAID Pact, World Fish Centre ndi sukulu zaukachenjede kugwirana manja ndi kumaimba nyimbo imodzi poteteza nsomba. Nyanja zonse za m’dziko muno zimayerekezedwa kuti zimatulutsa nsomba zoposera 50 000 tonnes pachaka, zomwe n’zochepa kwambiri kukwanitsa kudyetsera mtundu wa Amalawi. Motero sizodabwitsa kuti nsomba zina zimalowa m’dziko muno kuchokera kumaiko ena.

Kaamba ka kuchepa kwa nsomba, munthu mmodzi akumuyerekeza kuti akumadya makilogalamu anayi okha mmalo mwa makilogalamu 14 a nsomba pachaka. Izi zikupereka chithunzithunzi kuti ndi nsomba zochepa zimene zikumaphedwa m’nyanja ndi m’mitsinje ya dziko lino, motero n’kofunika kulimbikitsa njira zobwezeretsanso chiwerengero cha nsomba monga kutseka kwa nyanja komanso kuyambitsa ulimi woweta nsomba m’maiwe.

Kafukufuku wa bungwe la United Nations adapeza kuti kuonongeka kwa malo oberekeramo nsomba, kupha nsomba mopyolera muyeso pogwiritsanso ntchito zida zosakaza komanso kutayira zinyalala zapoizoni m’madzi kwadzetsa vuto la kuchepa kwa nsomba. n

 

Related Articles

Back to top button