Chichewa

Tsogolo la fizi silikudziwika

Listen to this article

 

Zenizeni pankhani yoti fizi yokwera m’sukulu za sekondale ndi sukulu za ukachechenjede za boma ipitilire kapena ayi zidziwika posachedwapa unduna wa zamaphunziro ukamanga mfundo, mneneri wa undunawu wauza Tamvani.

Iyi ndi nkhani yomwe Amalawi ambiri akumva nayo litsipa polingalira kuti mwezi wamawawu akuyenera kubowola matumba pankhani ya fizi zomwe posachedwapa unduna wa zamaphunziro udalengeza kuti zakwera.

Malingana ndi mneneri wa undunawu, Rebecca Phwitiko, undunawu ukudikira kalata yochokera ku Nyumba ya Malamulo yokhudza zomwe nyumbayi idamanga pankhaniyi.

Ophunzira a pasekondale ya Zingwangwa mumzinda wa Blantyre. Ena sapitiriza sukulu kaamba ka kukwera kwa fizi
Ophunzira a pasekondale ya Zingwangwa mumzinda wa Blantyre. Ena sapitiriza sukulu kaamba ka kukwera kwa fizi

“Sukulu zonse ndi mtundu wonse Amalawi udziwitsidwa za tsogolo la nkhaniyi posachedwa tikalandira kalata ya ku Nyumba ya Malamulo pa zomwe idamanga,” adatero Phwitiko.

Nkhaniyi idakambidwa m’Nyumbayi pamkhumano womwe wangothawu pomwe aphungu otsutsa boma adadzudzula kukwenza ka fiziku kuti kwabwera panthawi yolakwika.

Ngakhale padali zovuta zingapo, aphunguwo adakambirana nkhaniyo mpaka kugwirizana kuti ndi yofunika kuwunikidwa bwinobwino.

Mneneri wa Nyumbayi Leonard Mengezi adati pakadalipano sangapereke yankho lokhudza zomwe aphunguwo adakambirana poti nkhani ikakambidwa m’Nyumbayi imayenda mndondomeko zosiyanasiyana isadakhazikitsidwe.

“Mmene zidakambidwira m’Nyumba ya Malamulo muja, nkhaniyi imayenera kupita m’manja mwa komiti ya zamaphunziro kenako komiti yovomereza mfundo za boma isanapite kuunduna ndiye chitsekereni mkhumano mpaka pano sindidamve kalikonse,” adatero Mengezi.

Iye adati n’komuvuta kulondoloza nkhaniyi ndi makomitiwo kaamba koti anthu ali patchuthi ndiye sangapereke yankho logwira pokhapokha atabwerera m’maofesi awo tchuthi chikatha.

Nkhawa yaikulu fizi yokwerayi ikaloledwa ndi ana asukulu omwe alibe pogwira kaamba koti akhoza kulephera kuphunzira ngakhale atakhala anzeru.

Koma Phwitiko adati nkhani ya m’thumba isabweretse njengunje chifukwa pali ndondomeko zothandizira anthu ovutikitsitsa omwe sangakwanitse kulipira fizi zokwerazi.

“Tikudziwa kuti pali anthu ena ovutikitsitsa oti ngakhale fizi zisadakwere ankalephera kulipira, koma pali njira yothandizira anthu oterewa, monga ngongole kwa ophunzira a m’sukulu za ukachenjede komansothandizo la ulere kwa ophunzira a m’sukulu za sekondale,” adatero Phwitiko.

Iye adati ngakhale zili chonchi, pali ndondomeko yomwe ophunzira amayenera kutsata kuti apeze nawo mwayiwu pofuna kuti okhawo ovutikitsitsa ndiwo azipindula nawo.

“Kusankha anthu ovutikitsitsawa kumachitika m’maboma chifukwa ndimo muli anthu omwe amadziwa chilungamo cha anthuwo. Zimafunika mfumu ya kumudzi kwa munthuyo, ofesi ya DC ndi ofesi ya maphunziro (DEM),”adatero Phwitiko.Phwitiko adati ophunzira ovutika koma omwe ali ndi abale omwe ali ndi njira zopezera ndalama sadawaike m’gulu lopata ngongole kapena thandizo la fizi pofuna kupereka mpata kwa omwe alibiretu podalira.

Iye adati thumba lomwe kumachokera ndalama zothandizirali ndi loperewera kufikira aliyense n’chifukwa chake pali kusefaku.

“Tidachita dala kupereka ntchito yosefayi m’manja mwa maboma omwe ophunzirawo amakhala chifukwa ndiwo angadziwe wovutika weniweni chifukwa aliyense azifuna kupata nawo ndiye ife sitingadziwe kuti wovutika weniweni ndi uti,” adatero Phwitiko.Iye adati kulengeza za tsogolo la fizi zitengera kuti zokambirana zatenga nthawi yaitali bwanji.

Nkhaniyi ili apo, maofesi ambiri kuphatikizapo a m’boma ali patchuthi cha Khrisimasi ndi chaka cha tsopano.

Mabungwe omwe si aboma monga la mipingo la Public affairs Committee (PAC) ndi la zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) adati kukwenza fizi n’kofunika kutengera momwe chuma chikuyendera.

Mkulu wa bungwe la CSEC Benedicto Kondowe adati kukwenza fizi ndi njira yokhawo yotukulira maphunziro m’dziko muno polingalira kuti zinthu zidakwera ndipo ndi momwe chuma chikuvutira m’boma, mpovuta kutiboma palokha lingakwanitse kupereka ndalama zamaphunziro.

Kondowe adati vuto ndi nthawi yomwe boma lakwezera fiziyi polingalira kuti anthu sadakonzekere.

Iye adayamikira ndondomeko yothandiza ophunzira ovutikitsitsa kuti nawonso akhale ndi mwayi wa maphunziro. n

Related Articles

Back to top button