Chichewa

UDF yalonjeza za chiyambi chatsopano

Listen to this article

Chipani cha United Democratic Front (UDF) chanenetsa kuti chidzapitiriza kutukula ntchito za ulimi, maphunziro komanso umoyo wa anthu m’dziko muno chikalowa m’boma pa 21 May.

Izi zanenedwa Lamulungu pamene Atupele Muluzi amakhazikitsa manifesito ya UDF yomwe mutu wake ndi ‘Chiyambi Chatsopano.’

Mkamanga: Sakufotokoza bwino mwinano

Kumbali ya ulimi, manifesitoyo ikuti UDF idzamanga nkhokwe za m’madera zomwe zizidzasamalidwa ndi anthu amene akukhala kuderalo.

Koma katswiri pa ndale m’dziko muno, Emily Mkamanga watsutsa zakuthekera kwa mfundoyo ndipo wati chipanicho sichidafotokoze bwino mmene nkhokwezo zidzamangidwire.

“Sakufotokoza bwino madera amene adzapindule komanso mbewu zomwe chipanicho chikufuna kuti Amalawi azidzasunga m’nkhokwezo. Tonse tikudziwa kuti mbewu zambiri zimaonongeka kale m’nkhokwe, kodi zomwe anthu adzasungezi zidzasamalidwa bwanji?” adatero.

UDF yati idzasintha mbewu zina zomwe alimi amadalira pa chuma ndi chakudya monga fodya ndi chimanga kupita ku mbewu zina koma sichidafotokoze bwino za misika ya mbewuyo.

Chipanicho chati Amalawi adzapitiriza kugula zipangizo zotsika mtengo ngati angachisankhe kuti chilowe m’boma.

UDF yatinso idzaonetsetsa kuti pulogalamu ya zipangizo zotsika mtengozo ikupindulira anthu akumudzi komanso osaukitsitsa ngati njira imodzi yothana ndi njala.

Pa mfundo iyi Mkamanga adati ndondomekoyo sionetsa phindu lenileni kwa alimi chifukwa chinyengo chidalowererapo. Iye adati ndi bwino kuti ndondomekoyo ithetsedwe kuti pangokhala mtengo umodzi wa zipangizo za ulimi kuti aliyense azipindula.

Pa nkhani ya maphunziro, chipanicho chati chidzaonetsetsa kuti aphunzitsi alipo ochuluka makamaka m’sukulu zomwe zili m’madera a kumidzi komanso kuti atsikana azikhala pa sukulu mpaka atakwana zaka 15 ndi cholinga chothana ndi maukwati a ana.

UDF yati idzapanga ubale ndi mabungwe osiyanasiyana kuti athandizepo pa maphunziro awo.

Kumbali ya umoyo, chipanicho chati chidzamanga zipatala m’mizinda ya Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu poonjezera pa zipatala zazikulu zomwe zilipo kale.

Ngati zipani zina, UDF yalonjezanso kudzapeza njira zina za mayendedwe zomwe zidzalumikize dziko lino ndi maiko ena mu Africa.

Related Articles

Back to top button
Translate »