Nkhani

Uladi akaseweza zaka 5

Listen to this article

Khothi lalikulu ku Lilongwe Lachinayi lidagamula mkhalakale pandale Uladi Mussa kuti akasewenze zaka 5 pa mlandu wopotoza dala ntchito ya ofesi ya boma ndi chaka china chimodzi pa mlandu wogwiritsa ntchito ofesi ya boma kuti apindule.

Pogamula mlanduwo, woweruza Chifundo Kachale adati zilangozo ziziyendera limodzi kutanthuza kuti Mussa yemwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive Party (DPP) m’chigawo chapakati akasewenza zaka 5.

Mussa kubwerera kundende atapereka chigamulocho

Kadaulo pa ndale George Phiri wati zomwe zachitikazi zasonyeza kuti boma ndi lodziperekadi kuthana ndi katangale ngati momwe linkalonjezera pa nthawi ya kampeni ndipo wati lipitirize kuthamangitsa milandu.

“Mutha kuona kuti pamasiku 130 boma lagamula latsiriza milandu ikuluikulu iwiri wa Mzomera Ngwira komanso wa Uladi Mussa kutanthauza kuti atapitiriza chonchi ndiye kuti pakutha pa chaka mwina milandu 5 ikhoza kukhala itatha,” adatero Phiri.

Koma atatuluka m’khoti, Mussa adauza atolankhani kuti sakudziwa tchimo lomwe wachita kuti amunjate zaka zonsezo.

“Chiphuphucho chidali cha usipa? Zaka zonsezi bwanji ndalama za chiphuphuzo sindidazionepo ngakhale K1? Mukawafunse chomwe andimangira,” adatero Mussa uku akulimbana ndi asirikali a ndende ya Maula omwe amafuna akalowe m’galimoto.

Omuyimirira pa mlanduwo Paul Maulidi adati adapeza kale zofooka pa chigamulo chomupeza wolakwa ndipo akaunika bwino chigamulocho asadachite apilo.

“Ndalankhula kale ndi a Mussa ndipo andipatsa mphamvu zoti nditha kupitirira ndi ndondomeko ya apilo ndipo tayamba kale ndondomekoyo tateremu,” adatero Mauli.

Koma oyimilira boma pa mlanduwo Kamudoni Nyasulu adati ndi wokondwa ndi chigamulocho ngakhale iye amafuna kuti oweruza apereke chilango chokhwima kwambiri.

Popereka chigamulocho, Kachale adati Mussa sadatsate malamulo a ntchito pamene adali nduna ya boma zomwe zidachotsa chikhulupiriro mwa Amalawi ambiri.

Mussa amayankha milandu yofanana ndi yemwe adali mkulu waofesi yoona za anthu olowa ndikutuluka m’dziko mchigawo chapakati David Mkwanjana yemwe adalandira chilango chofanana ndi cha Mussa.

Pomugamula, Kachale adati nayenso adachotsa phwanya chikhulupiriro m’mitima ya Amalawi posatsata malamulo a ofesi ya boma yomwe amayang’anira.

“Ndapereka zilangozi kuti anthu ena ogwira ntchito m’boma atengerepo phunziro kuti azidziwa malamulo ndi choyenera kuchita pantchito ya ofesi yawo,” adatero Kachale.

Akuluakulu awiriwa adanjatidwa limodzi ndi nzika ya ku Burundi Peter Katasha yemwe khothi lidagamula kuti akasewenze zaka zinayi kundende. n

Related Articles

Back to top button