Chichewa

Ulangizi paulimi mu 2016

Listen to this article

Pamene tikulowa chaka chino mawa lino, ndi bwino tisanthule zina mwa nkhani zikuluzikulu komanso magawo amene tidakupatsirani mu Uchikumbe mu 2016.

Ulimi wa ziweto za mbalame
Alimi ena adabwekera kuti kuweta zinziri, nkhuku za mazira komanso za Mikolongwe, nkhanga. Alimi adafotokoza momwe ziwetozi zikuwapindulira. Mwa chitsanzo, mlimi wa zinziri adati sizichedwa kukula komanso zimapirira ku matenda. Amene akuweta nkhuku za Mikolongwe adati si zibwerera pamsika komanso kuweta kwake  nkosavuta. Kwa alimi a nkhanga, phindu lalikulu ndi lakuti zimaikira mazira ambiri—600 pachaka, zomwe si zingatheke ndi ziweto zina za mtunduwu.

Alimi adalimbikitsidwa kupewa matope m’makola awo

Malangizo paulimi
Kadaulo pankhani yosunga mbewu adalangiza alimi kupewa kusunga chimanga chawo m’nkhokwe za nsungwi poopetsa anankafumbwe. Iye adati chimanga chikatha, nankafumbwe amadya nsungwi ndipo mlimi akadzaika chimanga china nankafumbwe amapeza chochecheta. Alangizi enanso adatambasula za kufunika kukolola madzi pamene mvula yagwa komanso kuonetsetsa kuti akupeza mbewu ndi zina zofunikira paulimi nthawi yabwino. Adalangizanso alimi kukhala pagulu kuti asamavutike polandira ulangizi ngakhalenso kupeza misika.

Patsogolo ndi ziweto
Alimi a m’madera ena m’dziko muno adanenetsa kuti akusimba lokoma ndi ng’ombe za mkaka pamene adayamba kutsatira malangizo monga kusamalira makola, kufutsa nsipu, kubzala nsenjere, kuteteza matenda ndi zina zotero. Ndipo ena adati iwo koma akalulu amene akuthana ndi mavuto a kusintha kwa nyengo chifukwa chakudya chawo sichisowa. Kwa ena, kuweta nkhumba ndiye tsogolo labwino pomwe alangizi adanenetsa kuti kukhala ndi makola ouma, kudyetsa bwino, ndiye tsogolo lokoma la ulimiwu. Alimi ena adati koma mbuzi ndiye tsogolo labwino chifukwa sizivuta kudyetsa komanso matenda ndi ochepa.

Zina ndi zina
M’chakachi, akadaulo adapempha alimi kulimbikira pa mbewu zina za mtundu wa nyemba monga soya, nandolo, mtedza komanso nyemba zimene. Pambali poonjezera chonde m’nthaka, mbewuzi zimyenda malonda kwambiri pamsika ngati alimi azisamala bwino ndikutsatira ndondomeko zoyenera. Pofuna kuti ulimi wa mthirira upite patsogolo, akadaulo ena adati ndi bwino boma liyambe kulondoloza za ndondomeko ya ulimi wa mthririra ndi kuyikwaniritsa kuti alimi ngakhalenso dziko lino litukuke. Kudalinso malangizo a kafunika kwa manyowa a mitundu yosiyanasiyana amene amathandiza kuonjezera chonde m’thaka komanso kuteteza kuti isakokoloke ndiponso othandiza kuti alimi asaononge ndalama zambiri pogula feteleza. Ulimi wa kasakaniza ndi kasinthasintha nawo udalibimikitsidwa pomwe alangizi enanso adalimbikitsa kubzala mbande za mitengo. n

Related Articles

One Comment

  1. Chilungamo chokhachokha.Alimi ayenela kulimbikila ulimi wa ziweto powonjezera wa mbeu.Boma nalo liyenela kuwathandiza Alimi ndi ndalama zoyambira ulimi umenewu

Back to top button