Chichewa

Ulangizi wabala mwana ku Mulanje

Listen to this article

 

Njala yomwe yakhudza madera ambiri ikuvutanso m’boma la Mulanje komwe anthu akuyembekezereka kutuwa chifukwa cha mvula yanjomba yomwe adalandira nyengo ya mvula yapitayi.

Ngakhale njalayi yapereka mantha kwa ambiri, anthu a ku Mulanje West kwa T/A Juma, galu wakudayu wayamba kulambalala chifukwa cha ulimi wamthirira omwe wabonga kumeneko.

Mlimi kupatutsa madzi m’munda wa chimanga
Mlimi kupatutsa madzi m’munda wa chimanga

Monga akufotokozera Esther Makweya wa m’mudzi mwa Mlapa, langizo la alangizi awo ndilo labala zotsatira zabwino kumeneko. Alangiziwo akuti adawauza kuti akumbe zitsime ndi kuyamba ulimi wa mthirira zomwe zabereka mwana. Pano kuderali chimanga chili mbwee pamene ena akubzala, ena akukolola ndipo enanso atangwanika pamsika kukagulitsa chachiwisi.

Aggrey Kamanga ndiye wachiwiri kwa wokonza za mapulogalamu ku nthambi ya zamalimidwe ya Blantyre Agriculture Development Division (Bladd).

Iye adati nkhawa apachika kuti anthuwa angatuwe ndi njala chifukwa chomvera malangizo abwino.

“Tidawalangiza kuti ayambepo ulimi wa mthirira pokumba zitsime komanso pafupi ndi iwo pali mtsinje womwe suphwerapo. Pano aliyense ali kalikiliki ndi ulimi pamene ena tawalangiza kuti ayambiretu kupanga manyowa,” adatero Kamanga.

Ulimi omwe wayanja kuderali ndi wa chimanga, kabichi, tomato, anyezi, ndiwo za masamba kungotchula zochepa.n

 

Related Articles

Back to top button