Nkhani

Ulendo womaliza wa Grace Chinga

Listen to this article

Thupi la Grace Chinga yemwe adamwalira Lachitatu usiku liikidwa lero m’manda a HHI mumzinda wa Blantyre.

Thupi la Grace limayembekezeka kutengedwa kunyumba yachisoni ku College of Medicine dzulo masana ndipo lero cha m’ma 8 koloko thupi lake likuyembekezeka kutengedwera ku Robins Park komwe kukhale mapemphero komanso oimba anzake akhala akuimba pomukumbukira.

Adatisiya Lachitatu: Chinga
Adatisiya Lachitatu: Chinga

Malinga ndi malume ake a Grace, mbusa Isaac Mpasula, kuchokera ku Robins, ukakhala ulendo wa ku HHI komwe woimbayu akagone.

Pokambapo za chomwe chidapha Grace, Mpasula adati woimbayu amakhala ku Chilobwe ndipo sabata yatha iye adasamuka kukayamba kukhala ku Machinjiri ku Area 7.

Tsiku lomwe adangofika ku Machinjiriko, adaimba foni kwa mayi ake kuwadziwitsa kuti wafika bwino koma wangofikira kudwala.

“Adawauza kuti akudwala mutu, koma malinga ndi kufotokoza kwawo, sizimaonetsa kuti matendawo adali akulu, ndipo ife timati tipitako tsiku lina kuti tikaone komwe akukhala,” adatero Mpasula.

Iye adati pamene nthawi idali cha m’ma 6 koloko madzulo a Lachitatu, adaimbiranso foni mayi akewa kuwadziwitsa kuti Grace wakomoka koma apo amaimba ndi mwana wake wa Grace.

“Tisadanyamuke tidangomva kuti amutengera kuchipatala. Cha m’ma 9 koloko tikulandira uthenga kuti Grace wamwalira….” adatero mosisima.

Pamene timalemba nkhaniyo nkuti zotsatira za chipatala zisadatuluke kuti apeze chomwe chidapha woimbayu.

Mbiri ya Grace Chinga

Grace adabadwa pa 28 June 1978 ku chipatala cha Gulupu.

Grace ali moyo amati mtundu wawo udachokera m’dziko la Mozambique m’mudzi mwa Chinga. Pamene adalowa m’dziko la Malawi, bambo ake amakhala m’boma la Thyolo pamene mayi ake ndi a ku Chikwawa.

Iye wakulira ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre ndipo amapemphera mpingo wa Full Gospel womwe udayambitsidwa ndi bambo ake amenenso adamwalira.

Grace adakwatiwapo ndi Rodgers Moffat ndipo chithereni cha banja lake, iye sadakwatiwenso. Iye wasiya ana atatu: Steven, Miracle ndi Israel.

Kumbali yoimba, Grace adayambira ku kwaya ya kumpingo kwawo. Iye adalowanso gulu la All Angels Singers komanso Glad Tidings m’zaka za m’ma 1996.

Mu 2002 iye adatulutsa chimbale chake choyamba cha Yenda mu 2002 momwe mudali nyimbo zotchuka monga Uleke, Ndagoma, Timveke Maluwa ndi zina.

Kudziwika kwenikweni idali nthawi yomwe adatulutsa chimbale cha Ndiululireni momwe mudali nyimbo ngati Akadapanda Yehova, mu 2011.

Nyimbo zomwe anthu akhala akuimba m’sabatayi ndi monga Kolona yomwe mbali ina imati Ndinabwera ndi mission, Ndinatumidwa ukazembe, ntchito ikadzatha. Ndi pamene ndidzaweruke, Palibe ondileketsa ntchito yanga ili mkati, kufikira mwini wake adzanene kuti amen.

Grace wamwalira akuphika chimbale chatsopano momwe muli nyimbo imene adangoitulutsa ya Ndzaulula. Polankhula asadamwalire, Grace amati chimbalechi chituluka mu June mwezi womwe adabadwa.

Lero Grace wayalula monga mwa nyimbo yake ndipo maso a anthu akhale pa mwana wake Steven amene watulutsa nyimbo ya Udzandikumbuka.

Mmodzi mwa oimba amene adzamukumbuke Grace ndi Ethel Kamwendo chifukwa cha chinthu chimodzi chomwe Grace adamulonjeza Ethel adakali moyo.

“Adanena kuti ndikamakajambulitsa chimbale china, iyeyo adzandipatsa nyimbo ponena kuti nyimbo imeneyoyo ineyo ndi amene ndingathe kuimba. Zachisoni Grace wapita osakwaniritsa lonjezo lake,” adalira Ethel.

Related Articles

Back to top button