Chichewa

Ulima wa chimanga N’kutsatira ulangizi

Listen to this article

Katswiri wa zaulimi wa mbewu za m’gulu la masamba ndi zipatso ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Eric Chilembwe wati ulimi wa chimanga chachiwisi ndi wophindulitsa mlimi akatsatira upangiri woyenera.

Iye adati ulimi wa chimanga chachiwisi uli m’gulu la mbewu za mtengo wapatali chifukwa pa hekitala mlimi akachisamalira bwino ali ndi kuthekera kotulutsa chimanga chikuluchikulu chosachepera 10 000.

“Akachipezera misika yabwino n’kuchigulitsa pa mtengo wa K100 chimodzi ndiye kuti atuluka ndi miliyoni,” adatero Chilembwe.

Alimi amene amachita ulimiwu mwa nzeru amapha makwacha

Katswiriyu adati pamalo womwewo akachilekerera kuti chiume, amadzakolola chochepa, komanso kupeza ndalama zochepa akachigulitsa.

“Alimi kuti apeza phindu lochuluka akuyenera kumapatsana nthawi yolimira kuti chimanga chisamachuluke kwambiri pamsika.

“Mwachitsanzo, ena akatsiriza kugulitsa, anzawo azilowa kuti mtengo uzipitirira kukhala wabwino.

“Chinthu china chofunikira kwambiri n’choti alimi azisamalira chimanga chawo pothirira madzi ndi feteleza wokwanira, komanso kupalira kuti adzakolole chikuluchikulu, chopanda mipata choti munthu ukamuuza K200 chimodzi asanyinyirike,” adatero Chilembwe.

Iye adati mlimi ayenera kupezeratu misika ndipo ngati ali ndi mwayi asankhe misika imene chimanga chikugulitsidwa pa mtengo wokwera, komanso komwe amachikonda kwambiri.

“Mlimi azidziwa mbewu imene akubzala. Mwachitsanzo, ina imacha pakapita masiku 90. Choncho aziwadziwitsa anthu kuti pofika masiku awa chimanga chake chidzakhala chitacha.

“Alimi achimanga azisankha mbewu yocha msanga, komanso yobereka kwambiri kuti asamaononge ndalama pothirira nthawi yaitali. Akatero, adzaonjezera phindu lawo,” adatero Chilembwe.

Kaitane Shuga ndi mmodzi mwa alimi achimanga chachiwisi a m’boma la Blantyre.

Iye adati amapeza phindu lochuluka akalima chimanga m’mwezi wa March n’kugulitsa mu May kapena June.

Mlimiyu adati m’miyeziyi amapikulitsa pamtengo wa K100 chimodzi ndipo akamagulitsa choti anthu akadye kunyumba osati cha bizinesi chimafika mpaka K150 nthawi zina K200.

“Tikangolowa mwezi wa August kulekezera October chimatsika kwambiri chifukwa pamsika chimachuluka. Choncho timapikulitsa pa mtengo wa K50 chimodzi chachikulu pamene chaching’ono chimafika K30 chimodzi,” adatero Shuga.

Kuonjezera kutsika kwa mtengo wa mbewuyi m’miyeziyi, mlimiyo adati amavutika kuthirira chimanga chifukwa madzi amapezeka wochepa moti zotsatira zake mbewu zina sizibereka bwino kapena zimapserera makamaka chaka chimenecho mvula ikhala kuti idagwa yochepa.

Mlangizi wa mbewu wa m’boma la Dedza Madalitso Machira adathirirapo ndemanga kuti alimi ambiri a mbewu za m’madimba m’bomali sakonda kulima mbewuyi m’nyengo yozizira chifukwa choopa chiwawu.

Iye adati alimiwo amalima kwambiri nyengoyi ikadutsa zimene zimachititsa kuti chituluke nthawi imodzi.

“Amene amakwanitsa kulimbana ndi chiwawucho amapindula kwambiri chifukwa chimanga chimakhala chochepa pamsika,” adafotokoza motero.

Kupatula ndalama mlimi akagulitsa, Chilembwe adati chimanga chachiwisi chimapereka thanzi m’thupi la munthu kaamba koti chimakhala ndi michere yomanga thupi, shuga wothandiza kuti chitetezo cha m’thupi ku matenda chikwere, komanso kuti maso aziona bwino.

Related Articles

Back to top button
Translate »