Chichewa

Ulimi wa njuchi ndi ofesi yonona

Listen to this article

Kodi ulimi wa njuchi mudayamba liti?

Ulimiwu ndidayamba mu 2017.

Nanga chidakukopani n’chiyani?

Nditalingalira mozama ndidaona kuti ulimi wa njuchi sulira zinthu zambiri monga kulima, kugula feteleza, mankhwala ndi zina zochuluka kuti utheke. Chinthu china chomwe chidandikopa n’choti anthu masiku ano akukonda kugwiritsa ntchito uchi ngati chotsekemeretsa kusiyana ndi shuga malingana ndi zovuta zosiyanasiyana za m’thupi choncho ndidaona kuti msika wake ndiosasowa komanso ndalama yake ndiyolemelera.

Manduwa: Uchi wanga ndiika m’mabotolo

Kodi ulimiwu mukuuchitira kuti?

Ku Balaka, Lilongwe ndi Blantyre.

Kodi muli ndi ming’oma ingati?

Ndidayamba ndi ming’oma 10 koma padakali pano yafika 130. Ku Balaka kuli ming’oma 70, ku Lilongwe 50 ndipo ku Blantyre  10.

Nanga mumapeza uchi wochuluka bwanji pa mng’oma uliwonse?

Ikakhala miyezi yozizira ndimapeza  makilogalamu 30 pa mng’oma uliwonse pomwe nthawi yotentha umatsika kufika pa 20. Uchi umachuluka nyengo yozizira chifukwa tikamafika nthawiyi njuchi zimakhala zapanga chakudya chokwanira ndi cholinga choti zizingokhala m’nyumba mwawo muja ndikumadya. Chinthu china chomwe chimachititsa kuti uchuluke motere n’choti timakhala tikuchokera mu nyengo ya mvula yomwe zipangizo zogwiritsa ntchito popanga uchi monga madzi ndi maluwa zimakhala zochuluka.

Kodi mukagulitsa mumapeza ndalama zochuluka bwanji pa mng’oma umodzi?

Mng’oma umatulutsa K100 000, zikavutitsita K60 000.

Kodi misika ya uchi mumaipeza motani?

Msika wa uchi ndi wosasowa chifukwa alimi tilipo ochepa, koma akuugwiritsa ntchito ndiochuluka. Makampani ochuluka akhala akundipeza kuti ndiziwagulitsa uchi koma chifukwa cha kuchuluka kwa makasitomala anga sindingakwanitse. Chifukwa cha ichi, ndimaukonza, kuika m’mabotolo ndikumagulitsa ndekha kwa anthu.

Kodi upangiri wa ulimiwu mudauphunzira kuti?

Palibe yemwe adandiphunzitsa kapena komwe ndidakaphunzira ulimi wa njuchi. Ndili mwana ndimakonda kufula njuchi choncho lunsoli lidangokhala ngati landilowerera. Nditapita ku Lilongwe ndidaona anthu akuchita ulimiwu pogwiritsa ntchito miphika ndi mateyala ndipo nditaonetsetsa momwe amachitira maganizo woyamba kukhoma ming’oma adandibwerera. Ndidachita mwayi pamene bungwe la  World Vision lidandipatsa bisinesi yoti ndiwapangire ming’oma choncho nthawi imeneyo ndidaphunzira zinthu zambiri zokhudzana ndi ulimiwu.

Kodi ndi zinthu zotani zomwe zimafunika pa ulimiwu?

Zinthu zofunikira kwambiri pa ulimiwu ndi malo komanso ming’oma. Mlimi amayenera akhale ndi malo womwe ali ndi chilengedwe chokwanira monga mitengo ndi madzi. Ngati alibe malo woterewa koma akufunitsitsa atachita ulimiwu, akuyenera abzale mitengo yokula msanga monga mapapaya ndi moringa ndipo akhoza kuika chitsime kuti njuchi zizipeza madzi mosavuta. Malowa akuyenera akhale wotalikirana ndi nyumba za anthu mosachepera masentimita 100. Ulimiwu sulira malo aakulu chifukwa ndi ekala imodzi yokha mlimi ukhoza kuchitapo zazikulu.

Tafotokozani mwachidule momwe mumachitira ulimiwu?

Choyambirira, timapaka phula m’kati mwa mng’oma wathu, pakhomo ndi timitengo tomwe timasanja pamwamba pa ming’oma ija. Phula limathandizira kukopanga njuchi mu mng’oma muja choncho zikamva fungo lake, zimalowa n’kukhazikika. Tikachoka apo, timamangirira mng’oma wathu  ku nthambi za mtengo pogwiritsa ntchito mawaya omwe timawapakanso phula. Tikatero timati tamaliza koma timayenera tiziyendera ming’oma ija kufikira njuchi zitalowa ndikukhazikika. Zinthu monga nyerere, kangaude ndi mbewa zimadana ndi njuchi choncho chimodzi mwa icho chikapezeka mu mng’oma, palibe chomwe mlimi angaphule. Alimi akapeza zoterezi mu mng’oma, amayenera achotse.

Nanga mukamangirira ming’oma mumatenga nthawi yotalika bwanji kuti mukolole?

Timakolola pakapita miyezi itatu, koma nthawi zina imafika 6 malingana ndi momwe njuchi zikuchitira.

Kodi ndi mavuto wotani omwe mumakumana nawo ku ulimiwu?

Vuto lalikulu ku ulimiwu ndi kusowa kwa chilengedwe. Chifukwa cha ichi, ndikulimbana ndikubwezeretsa chilengedwechi ndicholinga choti ulimiwu upite patsogolo.

Nanga masomphenya anu ndi wotani pa ulimiwu?

Ndikufuna ndionjezere ming’omayi kuti ikwane 1 000. Cholinga changa n’choti ndizitha kugulitsa ku maiko akunja. n

Related Articles

Back to top button