Nkhani

Utsi ku Nam pamene ma Queens anyamuka

Listen to this article

Utsi ukufukabe ku bungwe loyendetsa masewero a ntchemberembaye la Netball Association of Malawi (NAM) kaamba kosemphana zochita pakati pa mphunzitsi wa timuyi Peace Chawinga-Kalua ndi bungweli.

Timu ya ntchemberembaye yomwe imangodziwika kuti Malawi Queens idanyamuka m’dziko muno Lachitatu m’sabatayi ulendo ku Sydney m’dziko la Australia komwe ikukapikisananawo m’chikho chapadziko lonse.queens4

Kugwebana kudayambika pamene zidadziwika kuti NAM idatumiza kale maina a atsikana amene apita ku Australia mosadziwitsa Kalua.

Malinga ndi Kalua, NAM idatumiza maina a osewerawo pamene iye asadawaitane kukampu kuti akachite zokonzekera.

“Ineyo ndi amene ndimayenera ndisankhe osewera amene achita bwino kukampuko. Koma zomwe zachitika nkuti NAM yasankha kale osewera ine ndisakudziwa. Nditatulutsa mndandanda wa osewera anga amene ndikuwafuna, iwo akana osewera ena amene ndawapatsa ndipo aika amene akuwafuna,” adatero Kalua.

Queens captured on departure at Chileka Airport in Blantyre.
Queens captured on departure at Chileka Airport in Blantyre.

Koma pamene amanyamuka pa bwalo la ndege la Chileka Lachitatu, nkhope za akuluakulu a NAM ndi mphunzitsiyu zimaoneka kuti sizikumvana zochita.

Chitsanzo, titamufunsa mphunzitsiyu zomwe akonzekera kukabweretsa kuchokera ku mpikisanowo, iye adati, “funsani amene akonzekera kukabweretsa zotsatira zomwe mukufunsazo. Ine sindingayankhe zimenezo,” adatero mphunzitsiyu uko akusonya a NAM kuti atifotokozere.

Koma titamufunsa pulezidenti wa NAM Rose Chinunda, iye adati sakuonapo vuto chifukwa ganizolo lidachitika atakambirana ndi wachiwiri kwa Kalua yemwe ndi Mary Waya komanso Griffin Saenda yemwe ndi wothandizira aphunzitsiwa kagwiridwe ka ntchito yawo.

“Tidafunsa anthu amenewa koma mphunzitsi yekha ndiye sitidamufunse. Ganizo lochotsa wosewera wina ndikubwereretsapo wina lidabwera titamva kwa awiriwa, ndiye palibe vuto komanso dziwani kuti majority rules [timamvera anthu ambiri popanga ganizo]” adatero Chinunda.

Komabe izi zakhumudwitsa kampani ya Airtel Malawi yomwe imathandiza atsikanawa. Mneneri wa kampaniyi Edith Tsilizani adapempha mbalizi kuti zikambirane ndikuthetsa kusamvanaku.

“Ndizodandaulitsa kuti pali chimkulirano chotere, koma ife tikupempha kuti akambirane ngati akufuna kuti tikabwere ndi zotsatira zabwino kuchokera ku ulendowo,” adatero Tsilizani yemwe kampani yake idapereka K7 miliyoni pa ulendowu.

Kalua amafuna atenge Ellen Chiboko wa Tigresses koma mmalo mwake NAM idachotsa dzina lake ndikuikapo Jean Chimaliro zomwe zadabwitsa.

Uwu ndi mndandanda wa osewera amene anyamuka ulendo ku Sydney; Mwawi Kumwenda, Joyce Mvula, Towera Vinkhumbo, Carol Ngwira, Sindi Simtowe, Takondwa Lwazi, Chimaliro, Grace Mhango, Lauren Ngwira, Thandi Galeta, Bridget Kumwenda ndi Martha Dambo.

Atsikanawa adatsimikiza kuti ngakhale pali kusamvana komabe ulendo wa ku Sydney akukamenya nkhondo.

Related Articles

Back to top button