Nkhani

Wa ganyu: Sesani m’nyumba

Listen to this article

Aganyu tadza pamaso panu bwana Kondi Msungama kaamba ka mpungwepungwe omwe wamanga nthenje kutimu ya Big Bullets.

Mphongo zikutsanzika kuti kuli bwino azikalima kusiyana ndi kukhalabe kutimuyi. Izitu zikuchitika pamene sipadathe chaka anthuwa atasankhidwa.

Bwana Msungama, kodi chikuchitika nchiyani? Aliyense akamachoka sakulephera kulankhulapo za akuluakulu ngati inu. Kodi vuto ndi amene akuchokawo kapena inuyo?

Nanga bwanji osakonza pamene palakwika kusiyana ndikumangolankhula zabwino m’mawailesi? Kukumvani mukulankhula pawailesi zikuonetsa kuti ndinu munthu woyera koma nanga bwanji anthuwa akusololokabe?

Timu ikuchita bwino koma mkangano wosatha, kodi izi sizikhudza timuyi pamene ikufunitsitsa itachita bwino m’mipikisano yake?

Monga manthu wa timuyi, bwanji osangolengeza kuti zinthu zasolobana ku Bullets kuti mwina anthu athandizirepo? Ngati kutere sikungathandize bwanji osakonza mbelewerere zomwe zikuoneka?

Titanena kuti mwalephera tilakwitsa? Poyamba timati ndi akomiti yakale amachititsa koma pano tiloze yani? Kodi aganyu mutitsimikizira bwanji kuti ulamuliro wanu umanga zinthu pamene zomveka zikungoti mbweee?

Nthawi ilipo bwana Msungama kuti mukonze zinthu. Koma dziwani kuti dziko likamasowa mafuta maso a anthu amakhala kwa mtsogoleri wa dziko kuiwala kuti kuli nduna yoona vutolo.

Vuto la anthu akuchokawo silingaoneke bwinobwino chifukwa onsewo ali pansi panu, kusonyeza kuti vuto lalikulu ndi inu chifuwa ndinu mutu wa Bullets.

Dzuwa silidalowe, konzani mavutowa uno ndi mmawa.

Related Articles

Back to top button
Translate »