Chichewa

Wa gulewamkulu atuluka pa belo

Listen to this article

Bwalo la milandu m’boma la Kasungu lapereka belo kwa munthu yemwe adayerekeza kuvala gulewamkulu ndipo akuganiziridwa kuti adagwirira mwana wa zaka 7 pomwe mwanayu amachokera kusukulu pamodzi ndi anzake ena awiri pa mtsinje wa Mkazimasika m’bomalo.

Gule wa mkulu

Apolisi a m’bomalo adagwira mnyamata wa zaka 16 ndi kumutsekera m’chitokosi sabata ziwiri zapitazo pomuganizira kuti ndiye adapalamula mlanduwo atavala gulewamkulu.

Ndipo mnyamatayu adadziwika chigoba chomwe adavala chitagwa pomwe adali mkati mogwirira mwanayo.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’bomalo Harry Namwaza, mnyamatayu adavomera kuti adapalamula mlanduwo pamaso pa woweruza milandu Damiano Banda.

Namwaza adati pakadalipano mnyamatayo wapatsidwa belo poyembekeza lipoti kuchokera ku nthambi ya boma yowona za chisamaliro cha anthu.

Malinga ndi malamulo oteteza ana m’dziko muno, mwana saweruzidwa pamlandu nthambi ya bomayo isanapereke lipoti lokhudza mwana amene wapalamula mlandu.

Koma mkulu wa nthambiyo m’boma la Kasungu, John Washali adati sakudziwa kalikonse za nkhaniyo ndipo sadalembe lipotilo.

Iye adati ndondomeko yake imafunika kuti mwana akapalamula asadapite kubwalo la milandu ofesi yake ilembe lipoti yomwe amapita nalo kubwalo la milandu ndipo woweruza amagwiritsa ntchito asadapereke chigamulo. n

Related Articles

Back to top button