Chichewa

Wa ku Mangalande anjatidwa atagwiririra wa ku Amerika

Listen to this article

 

Bwalo la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe lagamula nzika ya dziko la ku Britain Amrish Magecha kukaseweza zaka 8 mundende chifukwa chogwiririra nzika ya ku Amereka.

Kalata ya chigamulo chomwe chidaperekedwa pa 6 May, 2016 ndi Chief Resident Magistrate Ruth Chinangwa chasonyeza kuti nzika za maiko awiriwa zidakumana kumalo achisangalalo komwe zidamwa zakumwa zoledzeretsa.

Wodandaula adauza bwalo kuti Magecha adamutengera kumalo ogona alendo otchedwa Pine Lodge mumzinda wa Lilongwe usiku wa pa 8 August, 2015 komwe adamulowetsa m’chipinda n’kukhoma chitseko kenako n’kumugwiririra.

arrest

“Atakhoma chitseko ndidadzadza ndi mantha ndipo nditamupempha kuti atsegule adakana kenako n’kuyamba kundivula mogwiritsa ntchito mphamvu. Tidalimbana kwa kanthawi koma kenako mphamvu zidandithera mpomwe adapeza danga n’kundigwiririra,” adatero wodandaula.

Mugecha adavomera kuti adagonana ndi wodandaulayo koma adati zonse zidali zochita kupangana osati kugwiririra monga mmene adanenera.

“Tidatengana nkupita m’chipinda ndipo ine ndidakhoma chitseko pomwe iye adafikira kukhala pabedi kenako n’kuvula nsapato n’kugona. Nditakhala pamphepete pake, tidayamba kugwiranagwirana kenako adandiuza kuti ndivale kondomu.

“Ndidavomera ndipo nditavala tidayamba kugonana. Titamaliza ndidakataya kondomuyo n’kudzagona ndipo iye adandiuza kuti akufunika akapezeke kuntchito 7 koloko mmawa. Kutacha ndidakamutula komwe amagona ku Crown Lodge,” adatero Mugecha.

Koma patsiku loyambirira kuwonekera kukhoti, Mugecha adati: “Mundikhululukire pa zomwe zidachitika… Ndikupepesa kumtundu wa Amerika pazomwe ndidachita. Ndine nzika ya ku Mangalande ndipo ndikufuna kazembe wa Mangalande adziwe zimenezi. Ndidakwatira zaka 19 zapitazo ndipo ndili ndi mwana mmodzi.”

Pogamula mlanduwu, Chief Resident Magistrate Ruth Chinangwa adati mlandu wogwiririra omwe umatsutsana ndi gawo 132 la malamulo a dziko lino, chilango chake ndi moyo wonse kundende koma potengera mfundo zina monga momwe awiriwo adakumanirana ndi kutengana komanso kuti wolakwa sadapalamuleko, khothi limupatsa zaka 8 kundende. n

Related Articles

Back to top button
Translate »