Nkhani

Wa zaka 22 akufuna uphungu

Listen to this article
Machawa (kumanzere) limozdi ndi Mussa
Machawa (kumanzere) limozdi ndi Mussa

Timamva kuti achinyamata ndi atsogoleri a mawa, koma msungwana wa zaka 22 ku Nsanje wati akufuna kudzaimira chipani cha PP kudera la kumpoto m’bomalo.

Machawa Mcheka-Chilenje akuphunzira za chitukuko cha madera a kumidzi ndipo wati achinyamata asamaope ndale chifukwa ndi limodzi mwa magawo othandizira pachitukuko cha dziko lino.

Iye adati n’chifukwa akufuna kudzapikisana nawo ndi ena amene akufuna kudzaimira PP pa chisankho cha pa May 20, 2014 m’dera limene adaimirapo Gwanda Chakuamba komanso azakhali ake Esther Mcheka-Chilenje Nkhoma, yemwe adakhalapo wachiwiri kwa sipikala wa Nyumba ya Malamulo.

“M’dera lino muli mavuto a misewu, za umoyo, achinyamata ambiri sakupita kusukulu, zaulimi sizikuyenda chonsecho mtsinje wa Shire ndi mitsinje ina ili pafupi. Nthawi yoti achinyamata aziopa kuchita ndale idatha,” adatero iye.

Pomulandira, Nduna ya za M’dziko Uladi Mussa adati ichi ndi chitsanzo chabwino ndipo malamulo akumulola kutero.

“Malamulo oyendetsera dziko lino amaneneratu kuti ofuna kuimira uphungu akhale wa zaka 21 kapena kuposa apo. Iyeyu adakwanitsa zakazo ndipo tili ndi chikhulupiriro chonse kuti akwanitsa ntchito waiyambayo,” adatero Mussa.

Related Articles

Back to top button
Translate »