Chichewa

Wachiona ndani mu tnm

Listen to this article

Mpikisano wolimbirana ukulu mu 2016 TNM Super League wafika pamponda chimera—palibe amene akudziwikiratu kuti ndiye atenge mapointi ochuluka m’ligiyi.

Chaka chino zinthu zasiyana ndi zaka zina mmbuyomu. Monga chaka chatha, mmene kudatsala magemu 8 oti matimu asewere, aliyense adali atadziwa kale kuti Nyasa Big Bullets ndiyo itenge ligiyo.

Za chaka chino ndi zina, kwatsala magemu atatu kuti ligiyi ithe, komabe wotenga sakudziwika ngakhale kuti Kamuzu Barracks ndi Bullets akuoneka kuti ali ndi mwayi waukulu.

Umu ndi momwe ilili ligiyi. Matimu asanu—KB, Bullets, Blue Eagles, Silver Strikers komanso Mafco FC—ndiwo ali ndi mwayi wotenga ligiyi.

Bullets (malaya ofiira) kusewera ndi KB mmbuyomu

KB ili pamwamba ndi mapointi 52 pamene yasewera magemu 27. Timuyi yatsala ndi magemu atatu amene isewere ndi Dwangwa, Karonga ndi Eagles. Magemu onsewa, KB isewera koyenda.

Bullets, yomwe ikutsatira KB ndi mapointi 51 yaseweranso magemu 27. Iwo ndi omwe akuteteza chikhochi ndipo atsalanso ndi magemu atatu ndi Dwangwa, Civo ndi Eagles. Masewero onse akusewera pakhomo.

Eagles ili panambala 3 ndi mapointinso 51 itasewera magemu 27. Timuyi yatsala ndi magemu atatu ndi KB, Bullets komanso Mafco. Magemu awiri isewera pakhomo.

Achinayi ndi Silver ndi mapointi 50 nayonso itasewera magemu 27. Yatsala ndi Karonga, Wanderers ndi Mafco. Magemu awiri isewera pakhomo.

Pambuyo pa Silver pali Mafco ndi mapointi 47 m’magemu 27 ndipo yatsala ndi Eagles, Civo ndi Silver. Magemu awiri ali koyenda.

Ngati Bullets ingalondoloze mbiri yawo yosagonja pakhomo, ndiye kuti timuyi ili ndi mwayi wotenganso chikho cha ligiyi ngati ingadzagwetse Eagles, Dwangwa komanso Civo.

Komabe izi zingavutireko chifukwa Civo ndi Dwanga akumenya mpira woti asatuluke m’ligiyi komanso ikukumana ndi Eagles yomwe ikufuna kutenga ligiyi koyamba m’mbiri yawo.

Mwayi wa KB ndi wovutira chifukwa timuyi ili ndi mbiri yoipa kusewera kwa eni. Magemu atatu onse ikusewera koyenda, zomwe zikukaikitsa ngati ingakapambane onse.

Eagles ilinso ndi ntchito yovuta chifukwa ikuyenda kukakumana ndi Bullets pakwawo pamene simagonjapo komanso ikulandira matimu akuluakulu, Mafco ndi KB.

Silver ilinso ndi mwayi wotenga ligiyi chifukwa ikumenya ndi Karonga pakhomo pomwe ingapambane koma nkhondo ili pamene ikubwera pa Kamuzu Stadium kudzakumana ndi Manoma.

Koma kochi wa KB, Billy Phambala, akuti KB ndiyo itenge ligiyi chifukwa ili ndi njala yaikulu yonyamula chikho itakwapulidwa m’ndime yomaliza ya chikho cha Fisd.

“Magemu atatu amene tatsala nawo ndi osadetsa nkhawa, tikapambana ndi kutenga ligi,” iye adatero.

Timu yomwe ilepherane mphamvu ndi inzake, kapena kugonja pamatimu asanuwa atulukiratu pamndandanda wotenga ligi pokhapokha matimu enawonso zitawavuta.  n

Related Articles

Back to top button