Nkhani

Waganyu: Kulibe mipira yokonzekera zoona?

Listen to this article

Bungwe la FAM laletsa anyamata a Flames kuti asachite zokonzekera chifukwa ndalama palibe. Pofika dzulo zidali zisadadziwike ngati Malawi isewere ndi Mali komanso Ethiopia.

M’ndondomeko ya zachuma, Flames idalandira K70 miliyoni m’malo mwa K400 miliyoni. Pano ndalamayi yatha ndipo FAM palibe ingachite koma kulepheretsa zokonzekerazi.

Kodi apa tidzudzule boma kapena tiloze zala FAM? Vuto la mpira m’dziko muno si lachilendo ndipo ife sitikudzidzimuka kumva kuti boma lili chabechabe.

Misonkho yathu ikumakhala yokangobetsa osati kugwirira ntchito yomwe ifeyo tikufuna. Anthu akuzunzika kaamba kosowa mankhwala komanso zina. Apanso ndi izi kuti mpira tsopano ukupita pansi.

Masewero a mpira wamiyendowu ndiwodula kwambiri kusiyana ndi ena. Ife tikuona kuti Amalawi sitidakonzeke kuti tizipezeka nawo m’mipisano monga wa Afcon chifukwa mapeto ake tidzikhala ndi ndalama zosewerera gemu koma kulephera kupeza zokonzekera.

Sitikudziwa kuti anduna athu adziti chiyani apapa polingalira kuti adalonjeza kuti Flames ilandira ndalama zake mpaka kumaliza mpikisanowu?

Tikudabwa chifukwa tikayang’ana kuchipatala kuli mavuto, ku ulimi ndiye wosakamba, nako ku zamaphunziro ndi misewu ndiye mavuto a nkhaninkhani. Ndiye msonkho wathu uzigwira ntchito yanji?

Kapena ntchito ya misonkho yathu nchiyani? Kapena mufuna izingobedwa pamene ife tikuvutika? Ifetu zatikwana ndipo chiyembekezo chathu n’chakuti nduna ya zamasewero Grace Chiumia alankhulapo pa zomwe zikuchitikazi.

Related Articles

Back to top button