Chichewa

Wagolosale ndiye adandipatsa nambala yake’

Listen to this article

 

Anthuni, njira zophera khoswe n’zambiri koma chachikulu khosweyo afe basi.

Ena pofuna mkazi amachita kugwa m’ngongole kuti aoneke ngati, komatu nkhani ya mnyamata wodziwika bwino pa zautolankhani, Vincent Phiri, yemwe sabata yathayi wapanga chinkhoswe ndi okondedwa wake Mable Pikani, sidakhale choncho.

Mnyamatayu akuti kumangika pakamwa kudalipo mpaka adachita kufunsa nambala ya lamya pagolosale yomwe msungwanayo amakonda kugula zinthu ku Ndirande munzinda wa Blantyre komwe onse amakhala.

Akufuna kudzakhala banja lachitsanzo: Mable ndi Vincent
Akufuna kudzakhala banja lachitsanzo: Mable ndi Vincent

Iye adati ngakhale adatenga nambala ya lamyayo, sadayende moyera kufika pomwe alipa kaamba kakuti akatumiza timauthenga ta palamya namwaliyo amayankha mosonyeza kuti alibe chidwi. Koma pali khumbo, njira imakhalapo.

“Tsiku lina ndidaganiza zomuimbira ndipo ndidamupempha kuti ngati n’kotheka tikumane ndili naye mawu ndipo adandiyankha kuti ngati ndikufuna kukumana naye ndikampeze kwawo,” adatero Phiri.

Iye adati posakhalitsa ubale udayambika mpakana kugwirizana za banja chifukwa onse adaona kuti kudalembedwa kuti adzakhalira limodzi mpaka imfa.

Chinkhoswe chidalipo pa 28 November ku Kabula Hill m’boma la Blantyre ndipo zokonzekera zili mkati kuti chaka chamawachi adzamange ukwati woyera.

Vincent adati Mable ndi munthu yemwe ali ndi mtima wa mayi, wachikondi, wangwiro komanso wolimbikira ndi wodziwa chomwe akufuna m’moyo mwake.

Naye Mable adati Vincent ndi mnyamata wolimbikira, wamasomphenya ndinso wopanda mtopola ndi anthu.

Pano Vincent ndi woyang’anira za momwe malonda akuyendera kukampani ya Finca ndipo akuchita maphunziro a zosunga ndi kubwereketsa ndalama, pomwe Mable ndi namandwa wokonza zovala ndipo ali ndi malo akeake

osokeramo zovala. Koma onse awiriwa ndi atolankhani.

Vincent amachokera m’mudzi mwa Mkutumula kwa mfumu yaikulu Kwataine ku Ntcheu pomwe Mable amachokera m’mudzi mwa Kwachama, mfumu yaikulu Khongoni ku Kasiya m’boma la Lilongwe.

Iwo akuti masomphenya awo ndi odzakhala ndi banja lachikondi,

lachitsanzo, loopa Mulungu komanso lochilimika pazochitika. n

Related Articles

Back to top button
Translate »