Nkhani

Wailesi ya Dzimwe ikusowa thandizo ku Mangochi

Listen to this article

Nyumba youlutsira mawu ya Dzimwe Community Radio ku MonkeyBay m’boma la Mangochi yapempha thandizo lomangira ofesi komanso kugula zida zoulutsira mawu kuchokera kwa akufuna kwabwino.

Dzimwe, yomwe ili mkatikati mwa Lake Malawi National Park m’bomali ndipo ndi wailesi ya mudzi yoyamba m’mbiri ya dziko lino, idatsekulidwa m’chaka cha 1998.

Mkulu wa wailesiyi Hilda Phiri wati ngakhale ili yakale chomwechi, Dzimwe ilibe ofesi yakeyake komanso zida zoyenera zoulitsira mawu ndi makina a magetsi apadera [generator].

“Pakadalipano timagwiritsa ntchito mbali ina ya maofesi a Lake Malawi National Park. Tikupempha mabungwe ndi ena onse thandizo lomangira nyumba youlutsira mawuyi pakuti malo tinawapeza kale,” adatero Phiri.

Iye adatinso wailesiyi idatsegulidwa pofuna kutukula ntchito za umoyo ndi za chilengedwe m’madera a mafumu aakulu asanu andi anayi m’boma la Mangochi.

“Wayilesiyi yapindulira midzi yambiri ya kuno ku Mangochi komanso madera ena a ku Ntcheu ndi Balaka potukula umoyo ndi maphunziro,” iye adatero.

Mkuluyu adati wailesiyi ikuyenda chifukwa cha thandizo lomwe anthu okhala m’madera ozungulira amapereka.

Mmodzi wa omvera wayilesiyi ku Monkey Bay, Josephine Jenala, adayamikira ndi kuvomereza kuti yatukuladi maphunziro m’dera la kwawo kwa Chembe.

“Ndikunena pano ana ambiri akumapita kusukulu ndipo tikudziwa bwino zaumoyo. Timangodandaula magetsi akazima chifukwa wailesi nayo imazima,” adatero Jenala.

T/A Nankumba adatsimikiza za mavuto a wayilesiyi: “Dzimwe ikuthandiza kwambiri anthu m’dera lino. Koma mavuto a zachuma akufinya wailesiyo.”

Dzimwe idatsekulidwa ndi bungwe la UNESCO ndi boma ngati yongoyesera ya mudzi.

Related Articles

Back to top button
Translate »