Nkhani

Wapitadi Gwanda

Listen to this article

Ngati bodza Lachisanu lapitali walowadi m’manda Gwanda Chakuamba, mmodzi mwa amkhalakale pandale m’dziko muno.

Mmene chitanda cha malemu Chakuamba—yemwe m’maboma a Nsanje ndi Chikwawa kuchigwa cha Shire ankamutcha ‘Mbuya’ pomulemekeza chifukwa cha zabwino zambiri zomwe adakhala akuchitira anthu a kuchigwachi ali moyo, chimatsikira m’manda ku Chinyanje kwa T/A Mlolo, kuseri kwa nyumba yake yotchedwa ‘Zuwele Castle’—ambiri sadathe kuigwira misozi.

Maliro a Chakuamba adalandira ulemu wapadera poikidwa ndi asirikali a nkhondo a MDF
Maliro a Chakuamba adalandira ulemu wapadera poikidwa ndi asirikali a nkhondo a MDF

Ndi mitima yosweka ambiri adalira: “Wapita Mbuya, wapita Mbuya!” Amayi a Dorica a Muona Seventh Day Adventist adaimba mobwerezabwereza: “A Chakuamba ku Nsanje, a Chakuamba ku Chikwawa” kutanthauza kuti Chakuamba adali mwana wa maboma awiriwa.

Mizwanya ina yodziwika pandale yomwe idabwera kudzaperekeza ‘Mwana Mphenzi’ ndi mtsogoleri wakale Bakili Muluzi,  Sipika wakale Chimunthu Banda, Brown Mpinganjira, Sidik Mia, Kamlepo Kalua, Nicholas Dausi, Harry Thomson, Bazuka Mhango, akuluakulu a zipani za MCP, UDF ndi DPP ndi akuluakulu a boma motsogozedwa ndi mlembi wamkulu mu ofesi ya Pulezidenti ndi Kabineti George Mkondiwa, kungotchurapo ena pang’ono.

Inde kudali chinamtindi cha anthu—olira ndi ongoyang’ana, amipingo yosiyanasiyana ndi osapemphera omwe, koma onse okhala ndi cholinga chimodzi: kudzaperekeza munthu yemwe mbiri yake sidzaiwalika m’mbiri ya dziko la Malawi ngati mmodzi mwa anthu amene adamenyera ufulu wa dziko lino kuchoka m’manja mwa atsamunda kufikira lero lino pamene dzikoli lili paufulu wodzilamulira.

T/A Malemia amene adalankhula mmalo mwa T/A Mlolo pamaliropo, adati ngakhale akulira, koma ndi osangalala kuti kudera la chigwa cha Shire kudachoka munthu wodzipereka ndi wokonda anthu ake ngati Chakuamba yemwe dziko la Malawi silidzamuiwala.

“Sitidzapezanso Chakuamba wina kuno. Uyu ndiye adali weniweni; wangwiro, wachilungamo, wosaopa, mkhalakale pandale. Watiphunzitsa kukhululukirana ndi kugwirana manja ngati tifuna kuti dziko lathu litukuke.” Uku kudali kulira kwa Paramount Lundu.

Ena adayerekeza Chakuamba ndi malemu Nelson Mandela mtsogoleri wakale wa dziko la South Africa, pokhululukira chipani cha MCP, chomwe chidamangitsa n’kumuponya m’ndende kwa zaka 14, koma atatuluka kundendeko adalowanso chipani chomwecho n’kumagwira ntchito limodzi ndi omwe adamum-angitsawo.

Pa ichi, Malemia adati Chakuamba adali munthu wosasunga mangawa ndipo ankalankhula akaona kuti zinthu zikulakwika, zomwe zinkamuika m’mavuto nthawi zambiri.

“Chakuamba adali wokonda sukulu ndipo kuno waphunzitsa anthu ambiri,” Malemia adatero.

Ndipo ena mwa mafumu omwe Msangulutso udacheza nawo adati dziko lino lataya mkhalakale pandale yemwe adatengapo gawo lalikulu pothandizira kulitukula komanso yemwe adali wovuta kumumvetsa pakachitidwe kake mundale.

Inkosi Chindi ya m’boma la Mzimba idati idadzidzimuka itamva za imfa ya Chakuamba pawailesi Lolemba lapitali kaamba koti simadziwa zoti wakhala akudwala kwa kanthawi.

Chindi adagwirizana ndi mafumu anzake kuti Chakuamba adali wachitukuko.

“Adali munthu wabwino ngakhale munthawi ya ulamuliro wa MCP adali watinkhanza pang’ono. Paja adadzamenya mafumu kuno kumpoto pamsonkhano waukulu wa chipani mu 1973 ku Marymount mumzinda  wa Mzuzu,” adatero Chindi.

Iye adati mmodzi mwa mafumu omwe adapatsidwa makofi adali bambo ake chifukwa adakana kupereka ng’ombe ngati mphatso kwa Kamuzu.

Ndipo mfumu yaikulu Mkukula ya m’boma la Lilongwe idati sidzamuiwala Chakuamba chifukwa cha momwe adagwirira ntchito panthawi yothetsa bungwe la MYP.

Mkukula adati Chakuamba ngati mmodzi mwa akuluakulu a boma, adalolera kukambirana ndi kulithetsa bungweli bwino lomwe popanda zipolowe zambiri.

Mmodzi mwa otsata za ndale m’dziko muno, Humphrey Mvula, adati Chakuamba adamenyera ufulu wa dziko lino kuchokera nthawi ya atsamunda mpaka nthawi yomwe dziko lino lidathana ndi ulamuliro wa chipani chimodzi.

Malinga ndi Mvula, Chakuamba adali wolimba mtima ndipo sadali wosankha mitundu ngati momwe achitira andale ena omwe amakokera kwawo.

Mvula adati ngakhale Chakuamba sadapambaneko chisankho a mtsogoleri wa dziko lino, adatsala pang’ono kupambana m’chaka cha 2004 pomwe adaimira Mgwirizano Coalition.

Chakuamba adatsikira kuli chete Lolemba lapitali pachipatala cha Blantyre Adventist (BAH) mu mzinda wa Blantyre, naikudwa m’manda ndi ulemu wa asirikali ankhondo.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »