Chichewa

Wezzie: Chiphadzuwa chonenepa cha Mzuni

Sukulu yaukachenjede ya Mzuzu University idasankha chiphadzuwa chonenepa Loweruka sabata yatha pomwe adali ndi chisangalalo chawo cha Social Weekend. Mtolankani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere:

Tikudziweni

Ndine Wezzie Lwara ndipo ndimachokera m’mudzi mwa Thom Lwara, kwa Inkosi ya Makhosi M’mbelwa m’boma la Mzimba. Kwathu tinabadwa ana awiri ndipo ndine woyamba kubadwa. Ndili ndi zaka 20.

Manthu wa ziphadzuwa: Lwara (pakati)  ndi omutsatira ake
Manthu wa ziphadzuwa: Lwara (pakati)
ndi omutsatira ake

Mbiri yako ya maphunziro ndi yotani?

Ndidalemba mayeso anga a Fomu 4 pasukulu ya sekondale ya Ekwendeni, padakalipano ndikuphunzira zokopa alendo pa Mzuzu University. Ndili chaka chachiwiri.

 

Udayamba liti za uchiphadzuwa?

Kunena chilungamo aka nkoyamba kuchita izi. Mnzanga wina adangobwera kudzandiuza kuti ndikayese ndipo ndikhoza kupambana. Kuyesera ndi kupambana kudali komweko.

 

Udazilandira bwanji za kupambana kwako?

Sindikuchitenga chinthu chapafupi chifukwa sindidakonzekera kwambiri monga anzanga adachitira. Ndine wosanglala kwambiri makamaka chifukwa cha mphatso yomwe ndidalandira ya ndalama zokwana K50 000.

 

Ndiye ukuwauza chiyani makolo ako?

Kusukulu ya ukachenjede ndi komwe anthu amaphunzira ndi kuchita zinthu za msangulutso zambiri. Iyi ndi nthawi yomwe aliyense amene adapitako kusukuluzi amakumbikira kuti adasangalala.

 

Atsikana uwalangiza zotani?

Azilimbikira sukulu kuti adzafike malo ngati ano ndipo asamakhale ndi mtima odziderera. Pa atsikana amene tidapikisana, sikuti pasukulu pano atsikana onenepa ndife tokha ayi koma kumakhala kudzikaikira komwe kumatilepheretsa kuchita zinthu.

Related Articles

Back to top button