Chichewa

Wobwerera lili pululu amwaliranso ku zomba

Listen to this article

 

ZImene zachitika m’mudzi mwa Makoloni kwa T/A Mwambo ku Zomba masiku apitawa n’zoda mutu. Mayi wa zaka 28 amene adabwerera kumanda sabata ziwiri zapitazo bokosi la maliro lomwe adagoneka ‘mtembo’ wake litayamba kunjenjemera, wamwaliranso atangokhala kwa masiku anayi.

Mfumu ya m’mudzimo komanso woyandikana nyumba atsimikizira Msangulutso Lachiwiri lapitali za malodzawa ndipo ati anthu m’mudziwo akuganiza kuti zachitikazi n’zamasalamusi.

Wojambula wathu kufanizira ndi mmene zidakhalira tsiku limene Tamara Faliji ‘adauka kwa akufa’
Wojambula wathu kufanizira ndi mmene zidakhalira tsiku limene Tamara Faliji ‘adauka kwa akufa’

Patrick Matemba, yemwe adaona zododometsazi zikuchitika, adauza Msangulutso kuti Tamara Faliji adagwa kunyumba kwake masana a pa 11 August.

“Sitikudziwa chomwe chidachitika koma adangogwa. Tidamutengera kuchipatala cha Makwapala Health Centre komwe adatiuza kuti wamwalira,” adatero Matemba.

Monica Mbewe, namwino wa pachipatalachi yemwe adatsimikiza za imfayo poyamba, adauza Msangulutso kuti zomwe wodwalayo amaonetsa zidasonyeza kuti wamwalira.

“Adafika ali ndi moyo ndipo ndidayamba kumupatsa thandizo. Patatha mphindi 30 ndidaitanidwanso ndi amene amamuyang’anirawo kuti ndikaone zomwe akuchita. Panthawiyo amaonetsa zizindikiro zoti wawalira.

“Pamtima sipamagunda, thupi lidangolobdoka, diripi ya madzi ndi mankhwala idasiya kuyenda. Apa zidasonyeza kuti wamwalira moti ndineyo ndidalembera kuti wamwalira,” adatero namwinoyu.

Nyakwawa Makoloni potsimikiza za nkhaniyi, idati itamva za malirowo, idalamula anthu kuti ayambe kukonzekera zoika maliro mawa lake.

“Mawa lake adzukulu adakumba manda ndipo anthu a m’mudzimu adakhoma bokosi. Mwambo wa maliro utatha tidanyamula zovuta, ulendo kumanda,” idatero mfumuyi.

Koma Makoloni adati anthu adadabwa kuona bokosi likugwedera atangofika kumanda.

“Apa n’kuti mwambo wakumandako utangoyamba kuti titsitsire bokosi m’manda ndipo ndidalamula kuti bokosilo litsekulidwe.

“Titatsekula tidaona kuti ‘wakufayo’ akutuluka thukuta komanso amadziwongolawongola,” adatero Makoloni.

Iye adati mwambo udathera panjira ndipo adakwirira dzenje la mandalo nabwerera ndi woukayo kunyumba komwe kudaitanidwa ampingo wina wa Pentecost kuti amupempherere.

Pakulowa kwa tsikulo, akuti mayiyo adakwanitsa kudya phala koma movutikirabe.

“Amangovumata, kuti ameze ndiye kudali kovuta, komabe adadya pang’ono,” adatero Matemba.

“Kulankhula ndiye adasiyiratu ndipo pamasiku onsewo amangodya phala. Pa 16 August adadzuka wolefuka ndipo adasiya kudya. Kenaka mpamene timamva kuti wamwaliranso.

“Tidakhulupirira kuti ulendowu adamwaliradi chifukwa m’khwapa mudali mutazizira ndipo samatulukanso thukuta. Tidakaika maliro pa 17 August,” adatero Makoloni.

Koma mfumuyi yati ikuganiza kuti zomwe zidachitikazo zidali zamasalamusi ndipo akukhulupirira kuti imfa ya mayiyo wina adaikapo dzanja.

“Chilowereni ufumu zotere sindidazionepo. Ineyotu ndikuti ndidali pomwepo ndipo ndidadzionera zonsezi zikuchitika. Ndinadabwa nazo ndipo ndikukaika kuti zotere zingangochitika; alipo amene akukhudzidwa kuti mpaka mayiyu afe imfa yotere,” idatsindika mfumuyi.

Akuti malirowo atangochitika, adzukulu ndi anthu ena adamenya gogo ake a womwalirayo pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa yachilendoyo.

Makolo a malemu Tamala Faliji, yemwe wasiya mwana wa zaka 7, akuti nawonso adamwalira modabwitsa

Related Articles

One Comment

  1. Mmene anatsitsimukamo mumayenera kupita name ku chipatala akalandire drip ndi oxygen chifukwa mphamvu mthupi mwake munalibe ndinso mu brain mwake oxygen munalibe okwanira.
    Zinazi osamangoti ndi zamatsenga abale maiko achizungu zimachitika zoterezi abale inu. Mkutheka inali Bp or stroke Mwina simunkadziwa kuti ali nayo.Munthu anali moyo uyu koma wafa chifukwa cha kusazindikila chonde amzanga zoterezi zikachitika ganizo loyal a ndi kuchipatala basi.

Back to top button