ChichewaEditors Pick

Wofuna kugulitsa alubino achimina

Listen to this article

Bwalo la milandu la Mzuzu majisitireti lalamula Philip Ngulube, wa zaka 21, kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga kwa zaka 6 atamupeza ndi mlandu wofuna kuba msungwana wachialubino ndi cholinga chofuna kumupha.

Ngulube, yemwe adali mphunzitsi wodzipereka pasukulu yapulaimale ya Mongo m’boma la Mzimba, adagwirizana zomanga banja ndi msungwanayo, wa zaka 17, yemwe ankaphunzira pasekondale ya Mzimba.

Ngulube (akukokera kabudulayo) kutuluka m’khoti ulendo wa kundende
Ngulube (akukokera kabudulayo) kutuluka m’khoti ulendo wa kundende

Koma mphuno salota, Ngulube adali ndi maganizo ogulitsa msungwanayo kwa munthu wajohn chirwa malonda yemwe ndi mbadwa ya m’dziko la Tanzania.

Koma msungwnayo adapulumukira mkamwa mwa mbuzi mbadwa ya ku Tanzaniayo itakatsina khutu apolisi za malonda omwe Ngulube adali nawo. Apolisi ndi luntha lawo, adapita kwa Ngulube ngati ofuna kugula mualubinoyo.

Apa mpamene Ngulube adakwidzingidwa ndi unyolo zitapezekadi kuti amagulitsa mtsikana wachikondi wakeyu pamtengo wa K6 miliyoni.

Nkhani idapita kubwalo la majisitireti Gladys Gondwe komwe adazengedwa mlandu wofuna kuba munthu ndi cholinga chofuna kumupha, womwe adaukana.

Koma Lolemba lapitali, Gondwe muchigamulo chake chomwe chidatenga mphindi zisanu zokha, adalamula kuti Ngulube akagwire gadi kwa zaka zisanu ndi chimodzi.

Gondwe adati mlandu womwe amazengedwa Ngulube uli ndi chilango cha zaka zisanu ndi ziwiri.

Iye adati adaganiza zopereka zaka 6 ndi cholinga chakuti Ngulube adziwe kuipa kwa mchitidwe wofuna kuba munthu.

Woweruzayu adati n’zomvetsa chisoni kuti msungwanayo adasiya sukulu chifukwa cha kusowa mtendere ndi zomwe adachita Ngulube. Iye adati izi n’zotsutsana ndi malingaliro a mabungwe ndi boma polimbikitsa maphunziro a asungwana.

Wozenga mlandu wamkulu kuchigawo cha kumpoto, Christopher Katani, adati ndi wokondwera ndi chigamulo chomwe bwalo la milanduli lidapereka.

Iye adati zaka 6 ndi zokwana potengera kuti mlandu womwe amazengedwawo umayembekezereka kulandira chilango cha zaka 7.

Katani adatinso ndi wokhurira poti n’koyamba kumpoto bwalo lamilandu kutumiza munthu kugadi chifukwa cha mchitidwe wakuba anthu achialubino.

Ngulube polandira chilangochi, adaoneka kuti adali woyembekezera matherowo chifukwa sadaoneke kudodoma kulikonse.

Chithunzi: Ngulube akutuluka m’khoti ulendo wa kundende

Related Articles

Back to top button
Translate »