Chichewa

Woganiziridwa kuba khanda anjatidwa ku Mzuzu

Listen to this article

 

Mayi wina zake zada mumzinda wa Mzuzu atamugwira ataba khanda la psuu la mnzake pachipatala chachikulu cha Mzuzu sabata yatha. Koma make mwanayo pano akumwetulira chifukwa khanda lakelo lilinso m’manja mwake!

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Mzuzu, Cecelia Mfune, watsimikiza za kumangidwa kwa Mary Pundi Nyirenda, wa m’mudzi mwa Chisi, T/ A Mpherembe m’boma la Mzimba, yemwe akumusunga palimandi kundende ya Mzuzu komwe akudikirira kukaonekera kubwalo la milandu komwe akayankha mlandu woganiziridwa kuba khanda masiku akubwerawa.

Alinso limodzi: Wayisoni ndi mwana wake atapezeka
Alinso limodzi: Wayisoni ndi mwana wake atapezeka

Komatu khandali likadapita pakadapanda Maganizo Banda, mlonda wa kampani ya Stallion, yemwe ankalondera malowa usikuwo.

Banda adati adakhala tcheru ataona Nyirenda akutuluka ndi khanda kuchokera muwodiyo nthawi itatsala pang’ono kukwana 12 koloko usiku.

“Mayiyu adatuluka katatu konse kulowera wodi ya amayi apakati, yomwe ili moyandikana kwambiri ndi wodi ya makandayi, atanyamula khanda lomwe adalikulunga mushawelo yoyera. Amati kutuluka nkulowa.

“Apa ndidadziwa kuti china chake chasokonekera chifukwa kunja kudali kukuzizira ndipo mayi wanzeru sakadatuluka ndi mwana nthawi ngati imeneyo ndipo sindidamulole kuti atuluke,” adatero Banda.

Pocheza ndi

Msangulutso make khandalo, Mercy Wayisoni, wa zaka 27 yemwe amachokera ku Elunyeni m’boma lomwelo koma kumudzi kwawo ndi kwa Nazombe, T/A Nazombe m’boma la Phalombe, adafotokoza kuti adafika pachipatalapo Loweruka pa February 20 wopanda wina aliyense womudikirira.

Iye adati Loweruka lomwelo adakumana ndi mayi wina kukhitchini yemwe adamufunsa ngati ali ndi womudikirira ndipo iye atamuuza kuti adalibe aliyense womusamalira pachipatalapo, mayiyo adamupempha kuti akhale mnzake kuti aziphika ndi kudya limodzi osadziwa kuti adali zolowere n’kudyere mwana.

“Apa mpomwe ubwenzi wathu udayambira. Kwa masiku asanu ndi limodzi tinkadyera limodzi,” adatero Wayisoni koma adati adadabwa kuti Lolemba nthawi yochira itakwana Nyirenda adamuletsa kuitana wachibale aliyense kuti amuthandizire ndipo adamuuza kuti wachibale aliyense asadziwe zoti nthawi yake yochira idali itakwana kaamba koti iye alipo ndipo amuthandiza.

Wayisoni adati Nyirenda adali kumutsatira kulikonse komwe amapita patsikuli mpaka kuchipinda cha opaleshoni komwe adanamiza adokotala kuti adali wolandirira mwana ngakhale adokotalawo adamuletsa kulowa m’chipindamo.

Iye adati asadatuluke kuopaleshoniko, adokotala adamudziwitsa kuti adali ndi mwana wamwamuna.

Wayisoni adati adazizwa pomwe adadzidzimuka pakati pa usiku ndi kupeza kuti mwana wake salinso kumtima kwake koma mnzakeyo adali atamusunthapo.

“Adandiletsa kumuyang’ana mwana wanga ndi kundiuza kuti khandalo silidali langa koma lake kaamba koti langa lidapitirira. Izi zidandikwiyitsa ndipo ndidauza oyandikana nawo kuti Nyirenda wanditengera mwana ndipo adasinthitsa nsalu ine ndili mtulo,” adalongosola Wayisoni.

Iye adati nawo achipatala atamva kuti muwodimo mwauka mpungwepungwe adabwera ndi kutsimikiza kuti khandalo lidali la Wayisoni.

 

KUPEPESA

Tikupepesa chifukwa sabata yatha tidaika nkhani yolakwika ndipo tidati mayi ali pachithunzipa ndiye adaba mwana, koma uyu ndiye make mwanayo.—Mkonzi

 

Related Articles

Back to top button
Translate »