Nkhani

Wogwira ‘kumaso’ kwa mchemwali wake achimina

Listen to this article

Bambo wina wa zaka 32 ku Salima akunong’oneza bondo pano kaamba kosaugwira mtima mpaka kufuna kugonana ndi mchemwali wake.

Nkhaniyo ikuti bamboyo, a Gift Mwale, adapezeka adagwira maliseche a mchemwali wawoyo (yemwe sitimutchula dzina) mu usiku wa pa 20 February 2021.

Pali chitsimikizo choti mapulani a upandu a mkuluyo adayambira patali.

Malingana ndi wozenga milandu m’bomalo, a Pemphero Dzanjalimodzi, a Mwale adakapempha nawo ogona kwa mchemwali wawoyo atamva mphekesera kuti mkaziyo wathamangitsa mwamuna wake kubanjako pa kusamvana pa nkhani zina za m’banjamo alamu wawo achoka ku banjako kaamba ka kusamvana pakati pa awiriwo.

Mchemwaliyo atakana pempho lakelo, Mwale adabweranso n’kudzapempha mkeka ndipo mchemwaliyo adamukanizanso.

“Poona kuti mwayi wa zolinga zake ukunka ukuchepa, mkuluyo adamukoka mchemwali wakeyo n’kuyamba kumugwiragwira ku maliseche. Koma mchemwaliyo adakuuwa posagwirizana nazo ndipo anthu ozungulira adadza mwaunyinji omwe adamugwira mkuluyo n’kukamusiya m’manja mwa apolisi,” adatero Dzanjalimodzi.

Bwalolo lidaitana mboni zinai Mwale atakana mlanduwo pomwe adakaonekera koyamba ku bwalolo.

Woimira boma pa mlanduwo adapempha chilango chokhwima polingalira kuti wozengedwayo adachita monga wopanda umunthu komanso pofuna kubweza ena pa mchtidwewo.

Ndipo podandaula, Mwale—kudzera kwa womuimilira pa mlanduwo— adapempha bwalolo kuti limumvere chisoni chifukwa aka kadali koyamba kupalamula mlandu wa mtunduwo, komanso kuti ali ndi banja lomwe limayang’ana kwa iye pachisamaliro.

Koma madandaulo ake sadamveke chifukwa wogamula mlanduyo, a Joana Kwatiwani adatsindika kuti zaka zinai zomwe akakhale akugwira ntchito ya kalavula kundendeko imupatsa iye ndi ena phunziro la mphamvu.

Related Articles

Back to top button
Translate »