Nkhani

Woimba abedwa mumzinda wa mzuzu

Listen to this article

Anthu a m’dera la Mchenga-utuba mumzinda wa Mzuzu akukhala mwa mantha woimba wina wodziwika m’deralo atabedwa sabata yatha.

Woimbayu Dickson Banda yemwe amadziwika kuti Dick D anabedwa usiku wa Lachinayi sabata yatha ndipo adapezeka Lachiwiri.

Adapezeka ku Chimaliro: Dickson

Nawo aneneri a polisi ya Mzuzu a Paul Tembo atsimikiza kuti anthu ena anamutola mnyamatayo pamsewu m’dera la Chimaliro akungolira ndipo anakamutula kupolisi.

A Tembo anati izi n’zachilendo zangati izi kuchitika mumzindawo.

Potsatira nkhaniyi, Msangulutso unalankhula ndi bambo ake a Dickson a Moffat Banda omwe analongosola kuti mwana wawo ankapeka nyimbo tsiku lomwe anasowalo ndipo anawatsanzika makolo akewo kuti akukagula maunitsi kuti apeze bandulo ya Intaneti pasitolo yapafupi nawo yotumizira nyimbo anapekayo kwa mnzake.

“Koma akuti atafika panjira, anakumana ndi galimoto ya mtundu wa Voxy yakuda ndipo mmodzi mwa anthu omwe anali m’galimotolo anamuitana pomutchula dzina lake,” adatero a Banda.

Iwo anati atangoima Dickson adatsekedwa maso ndi pakamwa ndi chinsaru ndi kuponyedwa m’galimotolo.

“Watiuza kuti sakudziwa dera lomwe anampititsa koma anazindikira ali m’chipinda cha mdima wa dzaoneni chopanda mazenera,” anatero a Banda.

Iwo adati uku amamusunga ndi njala kupatula masiku awiri omwe munthu wina wovala zophimba nkhope anabwera m’chipindamo ndi kuyatsa magetsi komanso kumupatsa mpunga.

“Sanamuzindikire munthuyo chifukwa anadzibisa nkhope. Koma usiku wa Lachiwiri anakamutaya ku Chimaliro atamumanga komanso kumumenya. Anthu ena achifundo awiri ndiwo anamutola akungolira ndi kukamutula kupolisi,” iwo anatero.

Iwo anati apa analandira foni yoti apite kupolisi komwe anakamupezadi mwana wawoyo.

Malinga ndi a Banda apolisi anawatumiza kuchipatala komwe anakalandira mankhwala ndi kupatsidwa uphungu kuti apite kuchipatala cha St John of God akalandire uphungu chifukwa cha nyengo zomwe wadutsamo.

Mmodzi mwa anthu okhala nyumba zoyandikana ndi a Banda anati akhala akumusakasaka mnyamatayu kuchokera m’mawa wa Lachisanu sabata yatha ngati anthu okhudzika ndipo akubanja anakafika kuchipatala komanso kupolisi.

“Atangopezeka tonse tinakhamukira kubanjako kuti tikamve kuchokera pakamwa pake zomwe zinamuchitikira. Koma kunena moona mtima izi zatipatsa mantha chifukwa ndi koyamba kuchitika m’dera lathu lino ndipo tikukhala moyo wa cheucheu,” anatero bamboyo.

Nkhani za kubedwa kapena kusowa kwa anthu zayamba kumveka pafupipafupi m’dziko muno zomwe zikumapereka mantha kwa Amalawi.

Mwachitsanzo, mnyamata winanso anasowa mzinda wa Zomba chaka chatha ndipo anakapezeka m’dziko la Tanzania.

Pomwe anthu a mtundu wachialubino oposa 170 akhala akubedwa ndi kuphedwa komanso kuvulazidwa kuchokera m’chaka cha 2014.

Related Articles

Back to top button