Nkhani

Wokhapa mkazi wake amumanga

Listen to this article

Zina ukamva, kamba anga mwala. Bambo wina m’boma la Ntcheu wadzipha podziponya ku galimoto yothamanga atamukhapa mkazi wake kwa Kampepuza, Mfumu Champiti m’bomalo.

Bamboyu adamwalira Lamulungu lapitali.

Mayiyo adamukhapanso m’mutu

Apolisi m’bomalo atsimikiza za nkhaniyi ndipo adati a Samson Wailesi wa zaka 25, adakhapa mkazi wawoyo pomuganizira kuti amachita za dama ndi amuna ena.

Mneneri wapolisi m’boma la Ntcheu a Rabecca Kwisongole adauza Msangulutso kuti mkaziyo, yemwe ndi a Mwaiwawo Chiligo, adagonekedwa kuchipatala cha Ntcheu komwe akulandira thandizo.

“Awiriwo amakhala ku Liwonde ngati banja koma sizimayenda chifukwa cha kusamvana pa nkhani za kukhala ndi zibwenzi za mseri zomwe zimachititsa kuti azikhalira kumenyana,” adatero a Kwisongole.

Iwo adati mchitidwewu utapitilira, Chiligo adachokako ku banjako ndi kubwerera kwawo ku Ntcheu.

“Koma aWailesi adamutsatira mkaziyo ndi kumupempha kuti abwerere, koma adakana. Izi zidawakwiyitsa aWailesi ndipo adatenga chikwanje ndi kumukhapa mkazi wawoyo m’mutu komanso m’manja,” adafotokoza motero a Kwisongole.

A polisiwa adatinso atangomukhapa mkaziyu, aWailesi adamwa dziphe ndipo kuchoka apo adathamangira ku nsewu waukulu wa M1 komwe adakadziponya ku galimoto.

A Wailesi amachokera m’mudzi mwa Kaiya, Mfumu Yaikulu Ganya m’boma la Ntcheu.

Malinga ndi apolisi, m’boma la Ntcheu lokha, anthu 16 adadzipha kuchoka mwezi wa January kufika mwezi wa September chaka chino poyerekeza ndi anthu anayi omwe adadzipha m’nthawi ngati yomweyi chaka chatha.

Poona kuchuluka kwa anthu omwe akudzipha m’bomalo, apolisiwa alangiza anthu kuti azilandira uphungu banja likamavuta.

Komatu si boma la Ntcheu lokha komwe mchitidwe wodzipha wakula. Vutoli lili ponseponse m’dziko muno.

Kuchuluka kwa mchitidwewu, kwachititsa kuti akatswiri ena pankhani zakaganizidwe azitsekula zipatala zothandiza anthu omwe akuvutika m’malingaliro.

Komanso ena akumakhala ndi mikumano yosiyanasiyana yomwe akumapereka uphungu wokhudza mavuto a m’malingaliro.

Mwachitsanzo, pa October 30, pali mkumano mumzinda wa Lilongwe omwe wakonzedwa ndi cholinga chofuna kuthandiza anthu omwe akuvutika m’malingaliro.

Polankhulapo, yemwe wakonza nkumanowo a Pilira Ndaferankhande adati miliri monga HIV ndi Aids, Covid-19 ndi ina imabwera ndi mavuto otsatira ake.

“Mavutowa akabwera, amayi timakambirana kapena kudandaulirana pomwe abambo ambiri samasuka komanso alibe kokhutula mavuto awo.

“Choncho ambiri amayamba kumwa mowa mwauchidakwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo,” adalongosola motero a Ndaferankhande.

Iwo adati zotsatira za m’chitidwewu kumakhala kudzipha kuti angothana nawo mavutowo.

A Ndaferankhande adati abambo ambiri samasuka chifukwa chikhalidwe chathu chimawaonetsa kuti ndi amphamvu, zomwe zimachititsa kuti mavuto aja aziwasunga mumtima mpaka kubweretsa mavuto a m’malingaliro.

“Izi sizinasiye mbali chifukwa zikuchitikiranso kwambiri abambo omwe ndi a pantchito komanso a chuma,” adalongosola a Ndaferankhande. Iwo adati pamsonkhanowo, aitananso akatakwe a zaumoyo pa nkhani za m’malingaliro omwe atadzaphunzitse.

Related Articles

Back to top button
Translate »