Chichewa

Wonyozedwa ali moyo Alemekezedwa atamwalira

Listen to this article

 

Gogo wina ku Ntcheu, yemwe amagona pachisakasa chonga pogulitsira tomato abale ake akukana kuti agone m’nyumba yabwino, adalemekezedwa atamwalira ndipo siwa idali nyumba ya makono ya mmodzi mwa abale amamukana ali moyowo.

Batameyu James, wa zaka 67 wakhala akugona panjapo, samapatsidwa chakudya, amangodzionongera, ndipo mvula idakhala ikumuthera pathupi abale ake atatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangayerekeze kumuthandiza.

James m’chisakasa chomwe ankagona
James m’chisakasa chomwe ankagona

Gogoyu asadamwalire, adauza Msangulutso pa 25 December 2015 kuti ankagwira ntchito yaulonda ku Lirangwe m’boma la Blantyre koma pamene adabwerera kumudzi kwawo anthu sadamulandire.

“Ndinkagwira ntchito yolondera. Ndidapita kale ndipo sindingakumbuke kuti ndi liti. Mkazi wanga adamwalira komweko, ndipo ndidaganiza zobwerera kumudzi kuno komanso nthawi yomwe ndimabwera nkuti ndikudwala,” adatero gogoyu nthawiyo.

Koma ganizo lobwerera kumudzi kwawo kwa Howa, T/A Phambala silidakomere mchemwali wa gogoyu, Felisita James.

Gogoyo adafikira pamtengo, amagona pomwepo ndipo sabata isadathe akuti matenda adakula ndipo samayenda.

“Chimbudzi ndikupangira pomwepa chifukwa sindingakwanitse kupita kuthengo. Miyendo yafa komanso ndikuzizidwa kwambiri chifukwa zofundazinso zikumanyowa kukabwera mvula,” adatero akali moyo.

Titamufunsa Felesita chomwe sadamulandirire mbale wake, iye adati sakufuna kulankhula zambiri. Koma titamupempha kuti amulole gogoyu azigona m’nyumba mwake, iye adati: “Ngati alowe m’nyumbamu ndiye ine ndituluka.”

Kodi pali chifukwa chiyani chomwe akulangira mbale wawo? “Muwafunse kuti adachoka liti pakhomo pano. Ndiye andifune lero? nanensotu ndine wokalamba chifukwa iwowo ndi ine wamkulu ndi ine,” adatero iye.

Matenda atakula, gogoyu akuti adakomoka ndiye patsikuli adatengedwa ndi ena oyandikana nyumba kuti agone m’nyumba mwawo.

Chisakasa cha Jemusi ndipo kumbuyoko ndi nyumba ya siwa
Chisakasa cha Jemusi ndipo kumbuyoko ndi nyumba ya siwa28

Apa ndi pamene mudziwo udagwirizana kuti umumangire nyumba gogoyu koma malinga ndi nyakwawa Howa, izi sizidatheke.

“Timafuna tipeze kaye udzu koma mpaka amwalira anthu tisadakumanebe kuti timumangire nyumba gogoyu. Mbale wawo mmodzi wotchedwa Mkwaso ndiye adadzazika timitengoti,” idatero mfumuyo.

Pa 13 February akuti kudayamba mvula yosalekeza mpaka pa 15 ndipo mvulayinso akuti idamuthera pathupi gogoyu.

Gogoyo akuti adazizidwa kwambiri ndipo mmawa wa pa 15 adapeza kuti wamwalira. Koma abale adasonkhana ndi kuyamba mwambo wa maliro.

Koma chodabwitsa, thupilo akuti adalirowetsa mnyumba ya Felesita kuti anthu ayambe bwino kukhuza. Nsima yomwe wakhala akuisowa akuti idaphikidwa ndipo achibale adalira mosaleka.

Gulupu Mpochela idati anthu ena adakwiya kuona kuti banjali lidaganiza zolemekeza maliro kusiyana ndi munthu wamoyo.

“Gogogyu wakhala

akuvutika kwa nthawi yaitali. Adabwera kuno mu October mpaka wamwalira akugona panja opanda chakudya. Lero wamwalira ndiye amulowetsa m’nyumba ya malata komanso paphikidwa chakudya,” adatero iye.

Mpochela wati izi zakumukhumudwitsa ndipo aitanitsa banjali likamalira kulira malirowo. “Uku ndi kulakwa, kuzuza munthu wamoyo choncho komanso wokalamba ngati uyo sibwino. Ndawaitanitsa ku bwalo langa,” adatsimikiza Mpochela.

Gogoyu ali moyo adauza Msangulutso kuti ali ndi ana ku Lirangwe, koma pazolengeza za pamalirowo, abanja adati malemuwo sadasiye mwana ndipo mkazi wawo adamwalira.

Malinga ndi wachibale wina amene adakana kumutchula ndipo akukhala mumzinda wa Blantyre, malemuwa sadabereke mwana ndipo ana awiri amene amakhala nawo adali owapeza ndipo sadziwanso komwe anawo ali.

Nkhani zozuza anthu okalamba si zachilendo m’dziko muno. Posakhalitsapa, anthu ena ku Neno adapha anthu anayi okalamba powaganizira ufiti.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu okalamba la Malawi Network of Older Persons Organisations (Manapo), Andrew Kavala akuti ngakhale anthu akudziwitsidwa za ufulu wa anthu okalamba, koma akuchitiridwabe nkhanza zomwe wati nzachisoni. n

Related Articles

Back to top button
Translate »