Nkhani

Wotokosola mnzake diso akaseweza

Listen to this article

Khoti ya majisitireti ku Mangochi yalamula Joseph Mtambo wa zaka 25 kuti alipire K200 000 kapena akakhale kundende zaka zitatu chifukwa chovulaza mnzake.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ya Mangochi Amina Daudi wati Mtambo adavulaza Jacob Nambo amene amamukaikira kuti amayenda ndi mkazi wake iye akapita ku Joni.

An artist’s illustration of an arrested man

“Mtambo adapeza mauthenga achikondi mufoni ya mkazi wake. Iye adalemba uthenga kwa Nambo pafonipo kuti abwere kunyumba adzacheze pa 15 April. Atapita, Mtambo adamenya mnzakeyo ndi chitsulo ndi kumukolopola diso ndi waya,” adatero Daudi.

Nambo adagonekedwa pachipatala cha Mangochi, asanamutumize kuchipatala chachikulu cha Zomba. Chipatalacho chidatsimikiza kuti Nambo adapweteka m’maso ndipo sakutha kuona.

Woimira boma pamlanduwo, Grace Mindozo adapempha bwalolo lipereke chilango chokhwima kwa Mtambo chifukwa chovulaza mnzake. Koma Mtambo adapempha bwalolo kuti limumvere chisoni chifukwa ndi mutu wa banja lake.

Ndipo woweruza Augustine Mizaya adati kupereka chilango chokhwima monga adapemphera apolisi kungakhale kulakwa chifukwa Nambo adachitanso kumutokosola mnzakeyo, mpaka kupita kunyumba kwake.

Mtambo ndi wa m’mudzi mwa Mpinganjira, T/A Chimwala ku Mangochiko.

Related Articles

Back to top button
Translate »