Chichewa

Wotsatsa msuweni wake Amangidwa miyezi iwiri

Listen to this article

 

Ngati bodza, koma apolisi m’boma la Nkhotakota atsimikiza kuti bwalo la milandu la majisitireti lagamula kuti Bakali Chirwa, wa zaka 37, akagwire ukaidi wa miyezi iwiri kaamba kotsatsa msuweni wake, Hussein Banda, wa zaka 22, kwa msodzi wina wake pamtengo wa K550 000. Evance Green wa zaka 50.

Mneneri wa polisi m’bomali, Williams Kaponda, wauza Msangulutso kuti Chirwa, wa mmudzi mwa Mkumbira, kwa T/A Malengachanzi adatsatsa msuweni wakeyo kwa Evance Green, wa zaka 50, wochokera m’mudzi mwa Chilezi kwa Malengachanzi komweko, pa 8 February 2016, koma poyamba wotsatsidwayo ankaona ngati nthabwala.

“Green adatiuza kuti poyamba ankawona ngati akusereula chabe koma akuti adadodoma kuti patapita masiku atatu wotsatsayo adamupezanso nkumuuza kuti amafuna ndalama mwachangu ndipo amafunitsitsa bizinesiyo itayenda mwachangu,” adatero Kaponda.

Akadagulitsidwa: Banda
Akadagulitsidwa: Banda

Iye adati wotsatsidwayo adangouza mwini malondayo kuti amuyankhabe ndipo atasiyana adakanena kwa a nyakwawa Chilezi yemwe adamuuza kuti amuuze poti angakumane kuti malonda achitike, osadziwa kuti adamukonzera kampeni.

Kaponda adati tsiku lokumanalo, nyakwawa Chilezi adaitanitsa mboni mwachinsinsi kuti zidzamve zokha mwamseri za malonda achilendowo ndipo zina mwambonizo adali makolo awo a wotsatsa ndi wofuna kugulitsidwayo.

“Mudavuta mukhothi, Lachisanu lapitali [pa 11 March] woimbidwa mlandu ataona kuti pakati pa mboni padali makolo ake, ndipo adanenetsa kuti adamvadi momwe zokambirana za bizinesiyo zidayendera,” adatero Kaponda.

Wofufuza nkhani za polisi m’bomalo, Francis Banda, adati awiriwo atakambirana kwa kanthawi adagwirizana kuti agulitsane munthuyo pamtengo wa K500 000 ndipo kuti ayamba kupatsana theka kuti theka linalo adzapatsane popatsana malondawo.

Iye adati pofuna kuti wotsatsa malondayo asadzakane pamawa kuti walandira ndalama, adagwirizana kuti aitane mboni zoonerera akamapatsana ndalama zoyambirazo ndipo Chirwa adadzidzimuka kuona kuti mbonizo padali mayi a wogulitsidwayo ndi mchimwene wake (wa Chirwayo).

“Adangoti kakasi ndipo ife tidatsegula mlandu pomwepo mpaka adakalowa mukhothi momwe adalephera kuukana mlandu ndipo woweruza First Grade Magistrate Juma Chilowetsa adamupatsa miyezi iwiri kuti akagwire ntchito yakalavulagaga pa mlandu wochita zomwe zingasokoneze mtendere, zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 168 ya malamulo,” adatero Banda.

Green adauza Msangulutso lachinayi lapitali palamya kuti adali wodabwa ndi wamantha kumva munthu akumutsatsa malonda a munthu chonsecho sadamvekepo mbiri yochita malonda kapena masiramusi a ziwalo za anthu ndipo ichi ndicho chidamuchititsa kukadziwitsa a mfumu nkhaniyo isadafike pena.

Ankatsatsa msuweni wake: Chirwa
Ankatsatsa msuweni wake: Chirwa

“Tidakumana ndi kuchokera kunyanja ndipo adandilonjera n’kundiuza kuti adali ndi mawu. Nditampatsa mpata wolankhula adandiuza kuti adali ndi malonda koma malonda ake adali munthu. Ndidangoseka poona ngati macheza chabe,” adatero Green.

Iye adati kenako awiriwo adayamba kutsogozana mpaka pakhomo pake kenako wotsatsa munthuyo adatsanzika.

“Tsiku lina adadzandipeza pakhomo ndipo ndidamulonjera koma ndidadzidzimuka kumva kuti wabweranso ndi nkhani yomweyo ndiye ndidachita mantha kuti mwina kapena anthu akundiganizira zolakwika ndiye ndidakanena kwa a mfumu,” iye adatero.

Mkuluyu adati mfumu sidazengereze koma kumuuza kuti aoneke ngati akufunadi malondawo n’cholinga choti amukole wotsatsa munthuyo kuti nkhani ikapita kupolisi ikakhale ndi umboni ndipo zidachitikadi monga momwe mfumuyo idanenera.

Green adati wakhala akuchita usodzi kwa nthawi yaitali osagwiritsa ntchito chizimba chilichonse ndipo zimamuyendera bwinobwino komanso ali ndi makasitomala ambiri omwe amachita nawo bizinesi.

“Mwina amangoona momwe zimandiyendera n’kumaganiza kuti ndi mankhwala pomwe ayi ndithu, ndimachita chilichonse m’chilungamo ndi choonadi basi,” adatero mkuluyu.

Tidakanika kuyankhula ndi Banda, mnyamata amene adali pamalonda, kaamba koti tidalephera kupeza nambala ya foni yake.

Potsirapo ndemanga pachigamulochi ndi chilango chake, katswiri wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, wati olakwa ndi omwe adatsegula mlanduwo chifukwa kutsatsa munthu si mlandu waung’ono ngati momwe adauonera.

Iye adati oweruza milandu amagamula potengera zomwe auzidwa mukhothi, osati momwe ntchimolo lilili chifukwa amagwiritsa ntchito zomwe malamulo amanena.

“Wogamula mlandu amangomva zomwe ozenga ndi ozengedwa akunena nkupanga chigamulo, ndiye ngati ozenga apereka mlandu wopepuka chigamuloso chimapepukanso. Apa ozenga mlandu akadapereka mlandu waukulu kuti wogamula naye apereke chilango chachikulu,” adatero Kanyongolo.

Naye womenyera ufulu wa anthu, Timothy Mtambo, adati nzokhumudwitsa kuti anthu omwe amapezeka ndi milandu yoopsa amalandira zilango zopepuka, zomwe zimawapatsa danga lokabwereza mlanduwo.

Iye adati malamulo ambiri adapangidwa kalekale ndipo ndi ofunika kuunikidwanso kuti zilango zake zizifanana ndi chomwe walakwacho kuti azitengerapo phunziro, komanso anthu ena omwe adali ndi cholinga chopanga zomwezo asamapangire dala.

Related Articles

Back to top button
Translate »