Nkhani

‘Youth Week’ ibwereredi —Achinyamata, mafumu

Listen to this article

 

Mtsogoleri wa achinyamata pa ndale wa bungwe la Young Politicians Union Clement Mukuwa wati ndi wosangalala ndi ganizo la boma lofuna kukhazikitsanso sabata ya achinyamata (Youth Week) chifukwa likugwirizana ndi zomwe achinyata adaika pamndandanda wa zolinga zawo.

“Tili ndi mndandanda wa zomwe tikufuna achinyamata atamachita ndipo chimodzi mwa izo ndi kugwira ntchito modzipereka ndiye tikakumbuka zomwe Youth Week inkachita, zikugwirizana ndi mfundo imeneyi,” adatero Mukuwa.

Kudikira kuti boma likonze: Munthu kuoloka movutikira paulalo woonongeka
Kudikira kuti boma likonze: Munthu kuoloka movutikira paulalo woonongeka

Phungu wa kumpoto cha kummawa kwa boma la Mchinji, Alex Chitete, ndiye adayambitsa nkhaniyi m’Nyumba ya Malamulo pomwe aphungu amaunika momwe chuma cha dziko chayendera pamiyezi isanu ndi umodzo (6).

Phunguyu adapempha boma kuti likhazikitsenso sabata ya achinyamata monga zidalili m’nthawi ya ulamuliro wa malemu Dr. Hastings Kamuzu Banda pomwe achinyamata m’dziko muno adali ndi sabata yogwira ntchito zachitukuko m’madera awo pofuna kuwaphunzitsa za ubwino wogwira ntchito modzipereka potukula dziko lawo.

Iye adati panthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi achinyamata ankatenga gawo lalikulu pachitukuko kusiyana ndi masiku ano pomwe kuli ntchito zogwira ndi chiyembekezo cholandira dipo yomwe akugwira ndi anthu akukuluakulu.

Poyankhapo, nduna ya zantchito Henry Mussa adati ganizoli si loipa koma silokakamiza ndipo m’mapulani a boma muli kale ndondomeko zomwe akuti achinyamata azipatsidwa mpata kutenga nawo mbali pantchito zina.

Iye adati mundondomekoyi, ntchito zina zomwe zizigwiridwa ndi zachitukuko monga momwe zinkakhalira m’nyengo ya Youth Week kalelo.

“Tidayankha kale pankhani imeneyo kuti si zokakamiza koma ndondomeko ilipo kale moti pompanopompano ziyambika,” adatero Mussa.

Mukuwa adati ngati mtsogoleri wa achinyamata pandale akhoza kukhala wokondwa anthu atadziwitsidwa ubwino wa Youth Week ndi zolinga zake kuti mtima wogwira ntchito wodzithandiza posayembekezera malipiro ubwerere mwa Amalawi.

Katswiri pa mbiri ya dziko lino, Desmond Dudwa Phiri (DD Phiri), ndi mafumu angapo akuluakulu ati ganizo lokhazikitsanso sabata ya achinyamatali ndi lofunika kwambiri pachitukuko cha dziko la Malawi.

DD Phiri adati Youth Week ndi nyengo yomwe achinyamata ankatengapo mbali pachitukuko chosiyanasiyana ngati nzika za dziko mwaulere ndipo izi zinkathandiza kutula midzi ndi madera omwe ankakhala.

“Nthawi imeneyi achinyamata ankakhala otangwanika kwambiri pantchito zachitukuko monga kukonza misewu, milatho, zipatala, sukulu ndi zina m’madera mwawo mwaulere ndipo zinthu zinkayenda,” adatero mkhalakaleyu.

Iye adati ntchito ngati zomwezi, pano zimalira bajeti yaikulu kuti anthu agwire, mapeto ake ndalama zikasowa, zitukukozi zimayamba zaima kwa nthawi yaitali, zinthu nkumapitirira kuonongeka.

“Youth Week inkakhalako chaka chilichonse nyengo ngati ino ya Pasaka ndipo tinkadziwiratu kuti misewu yonse yoonongeka, milatho, zipatala, sukulu ndi nyumba za aphunzitsi zomwe zikuonongeka zikonzedwa.

“Pano ntchito ngati zimenezi zimalinda ndalama za m’bajeti kuti anthu kapena makontirakitala azigwire. Ngati ndalamazo palibe, ndiye kuti zinthuzo zizingopitirira kuonongeka mpaka ndalama zidzapezeke,” adatero DD Phiri.

Mkuluyu adati Youth Week idatha m’dziko muno mutabwera ulamuliro wa zipani zambiri poganiza kuti idali nkhanza kwa anthu (thangata) ndipo mmalo mwake boma lidasenza lokha udindo wogwira ntchito zachitukuko.

Iye adati koma anthu sankaona Youth Week ngati thangata ndipo ankagwira ntchito modzipereka ndi umodzi mpaka pomwe adauzidwa kuti ndi ‘thangata’.

Mkulu wodziwa za mbiri yakaleyu adati maiko ambiri omwe ndi otukuka pano adayamba ndi eni ake kudzithandiza ndipo boma linkangobwera pambuyo kudzawonjezera pomwe paperewera.

Mfumu yaikulu (T/A) Maseya wa ku Chikwawa akugwirizananso ndi ganizoli ponena kuti achinyamata amaphunzira ntchito zosiyanasiyana panyengoyi chifukwa amasakanikirana ndipo omwe adali ndi luso amagawira anzawo pogwira ntchitozo.

Iye adati kudzera m’njira imeneyi, achinyamata amakula ndi mtima wokonda ntchito ndiposo zimawathandiza kukhwima m’maganizo kuti paokha akhoza kupanga chinthu chooneka popanda kuyang’aniridwa.

“Zidali zokoma kwambiri moti zitati zayambiranso zikhoza kukhala bwino kungoti nzofunika kuti poyambitsapo aunike bwinobwino kuti ntchitozo angazigawe motani potengera zaka kuti zisakolane ndi nkhani yogwiritsa ana ntchito yoposa msinkhu wawo,” adatero Maseya.

Inkosi Chindi ya ku Mzimba idasangalalanso ndi ganizoli ponena kuti nyumba zambiri zophunziriramo, zokhalamo aphunzitsi, milatho ndi misewu zomwe pano zili ngati bwinja zikhoza kukonzedwa mosavuta.

“Chitukuko cha kudera ndi udindo wa anthu okhala kudera limenelo ndiye anthu atafotokozeredwa bwinobwino phindu lomwe angapeze kuchoka muntchito zachitukuko cha Youth Week, sindikukhulupirira kuti angawiringule,” adatero Chindi.

Iye adati munyengoyi, achinyamata amagwira ntchito zosiyanasiyana monga kulambula misewu, kukonza milatho, nyumba za aphunzitsi ndi zitukuko zina uku akutayitsa nthawi ndi macheza.

Naye T/A Mkanda ya m’boma la Mchinji idati ana ambiri masiku ano amalephera kupita kusukulu nyengo ya mvula kaamba kolephera kuoloka mitsinje chifukwa chodikirira kuti boma likonze milatho.

Related Articles

Back to top button
Translate »