Chichewa

Za Jessica Bwira ndi zina

Listen to this article

 

Mvula idagwa tsikulo pa Wenela si ndiyo. Kaya inkachokera kuti kaya!

Abale anzanga, musandifunse za Jessica Bwira, Mwano Mkangama komanso Pierre Chamkhwatha. Zoziyamba dala! Kodi mwati foni ingalande ufumu wa Mose?

Zidaliko pa Wenela tsikulo.

“Inetu za WhatsApp ndi zina zotero ndilibe nazo gawo. Komabe ndikudabwa kuti asirikali awa pa Wenela adayamba liti kulowetsa anthu kozizira pofuna kuwachenjeza. Zachilendo ndithu,” adatero Abiti Patuma.

“Ukungonena iwe. Kuchezatu kwaphweka ndipo kwatchipa. Kunena zoona, ngakhale Male Chauvinist Pigs akudziwa bwino lomwe kuti ana a Farao adagwiritsa ntchito kwambiri foni kuthamangitsa Farao ku ma pyramid a ku Gizeh. Umamudziwa Cheops iwe? Nanga chidathyola mphuno ya The Great Sphinx n’chiyani? Sindikukambatu za Great Sphinx of Quartz,” adatero mkulu adali naye tsiku limenelo.

Kaya ndi sukulu kaya ndi chiyani koma sindikudziwa kuti ankakamba chiyani. Iye ankalankhula mokuluwika ngati Moya Pete.

“Zonse zili apo, apatu zangosonyezeratu kuti ku Male Chauvinist Pigs kuli amthirakuwiri. Nanga achina Niko adziwa bwanji izo amakambirana kuchipinda cha foni?” adafunsa Abiti Patuma.

“Zoona. Koma mpaka kuwamanga kuti awachenjeze? Chadza ndi yani?” adafunsa mkulu uja.

Nkhani imene idatifika pa Wenela idali ya kutengedwa kwa Jessica, Mwano ndi Pierre. Iyitu ndiyo nkhani idaphimba za mneneri Bushi Minor amene waletsedwa kugawa nandolo ndi chipere chifukwa Moya Pete wakhuta kwambiri ndipo sakumvanso njala. Sakufunanso kumva zakuti wina wagona ndi njala.

“Koma ndiye zinaliko! Khoba ng’azing’azi kuchita zawo zija pa Lilongwe apa! Mumayesa masewera?” adailowa nkhani Gervazzio.

“Kodi Moya Pete simesa adatiuza kuti zomangana za ziii pano pa Wenela ayi? Nanga apa alonda ake akuti chiyani?” adafunsa mkulu adali ndi Abiti Patuma.

“Adakuuzani zomangana zokhazo? Musaiwaletu kuti adabweretsa ana ake aja kuti mukhulupirire kuti iyeyo sadagwe mumtengo wa papaya. Lero anawo angabwerenso pano pa Wenela kuti adzafe ndi njala ngati gogo uja?” adafunsa Abiti Patuma.

Langatu lidali khutu chabe. Mlomo wanga udali womangidwa ndi loko ngati sefa ya ku Reserve Bank.

“Ndiye ndikumva kuti mayi wathu amupatsa tsamba lapamwamba, ung’anga wodziwa kusesa ndi kukolopa zimbudzi,” adaisintha nkhani Abiti Patuma.

“Simukudziwa inu. Pamene mukubwebweta za njala simukudziwa kuti iyi ndi njira yothetsera phokosolo? Zinyalala momwe zachulukira pano pa Wenela wina nkumalandira nazo masamba? Koma abale, misalatu yachuluka pano pa Wenela,” adatero mkulu uja.

Abale anzanga, musandifunse za zinyalala pano pa Wenela. Nokha simukuona? Fungo lochoka mumtsinje wa Mudi silitseka mfuno zanu? Mfemvu–ndikunena mphemvu–sizinaberekane phwamwamwa pano pa Wenela?

“Tsono ngati akulandira tsambali, amene amasesa mumsewu awapatsa chiyani?” adafunsa Abiti Patuma.

“Pamene mukuti kuli njala, simunamve kuti tikutseguliranso msewu uja adatsegulira Adona Hilida? Simudamve tikutseguliranso msewu uja adausintha dzina Mpando Wamkulu? Zochita kuphiri ziliko zambiri. Zikuyenda pa Wenela,” adatero mkulu uja, uku akuvula malaya ake kuti ationetse T-shirt yake ya mtundu wa thambo pali zitsononkho zitatu.

Inu! Inu! Inu!

Gwira bango, upita ndi madzi! n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »