Chichewa

Za maukwati, mabanja

Listen to this article

Money is gooooood

Musayense njerego, awa ndi mawu ochokera munyimbo ya Miracle Money ya mnyamata wodziwa kuimba nyimbo zauzimu, Onesmus. Poyamba, ndinkamva ngati akuti God is good!

Iyitu ndi nyimbo yauzimu imene imakamba za ndalama zozizwitsa zimene zingapezeke m’kachikwama kanu kapena kubanki modabwitsa. Akhoza kukhala mamiliyoni. Si za kashigetitu!

Major do it! Major do it!

Pamenepanso ndimayesa akuti God do it! God do it! Zoona, ambiri timalambira dzuwa m’malo molambira wolenga dzuwalo.

Musayambe kundinena kuti ine zindikhudza bwanji. Inetu ndimakhulupirira kwambiri Mateyu 7 vesi ya 1: Osaweruza ena chifukwa ndi mlingo umene uweruzira ena, nawenso udzaweruzidwa. Ndine ndani ine, kapunthabuye, kafucheche, kwakwananda ndipo ndikadakhala nsalu bwenzi ndili kilimpulini.

Sindinakumalizireni nkhani ija sabata yatha. Tidaika zovuta kumanda ena pafupi ndi pa Wenela. Ubwino wake, wotisiyayo adali atagula kale puloti yake kumasanoko.

Titaika zovutazo, mkulu wina adanditengera pambali: “Tade kodi panthumbira paja anaikapo maluwa chifukwa chiyani? Kodi malemuwo adali kalipentala? Nanganso anaikapo mtanda wa thabwa, kodi malemuwo adali kalipentala? Sindikaika kutsogoloku adzawaka mandawo ndi simenti ndi quary ngati malemuyo anali kontilakita.”

Sindidamuyankhe.

Titafika malo aja timakonda pa Wenela, kudatulukira mkulu wina atanyamula zibonga ndi mikondo.

“Tiwaphe basi! Amenewa aphedwe basi! Ndithu pa filling station munthu angathire mafuta kotulukira utsi?” adafunsa mkulu wa zikwanjeyo.

Dzina lake ndi Nike Masonda, mnzake wa Adona Hilida ku Polisi Palibe. Tsono akadati alowe kumpanda ku Sanjika bwenzi ataika malamulo wotani mkuluyo?

Zidandipita.

Koma Abiti Patuma akuoneka kuti adazitolera. “Pezani zina zokamba. Ndimayesa muzinena za chimbudzi choyendayenda cha Moya Pete. Zomwe mukunenazo tidazimva kale. Ati Mugabe adawauza akwatirane ndipo mubadwe mwana, apo ayi awakhiya pakhosi,” adatero.

art

“Ndipo izo zili apo, tidamvaponso za wina amene ankanena kuti satana akadakhala wa maganizo otere bwenzi atapusitsa Adam osati Hava kuti adye chipatso cha pakati pamunda. Koma zochitika kuchipinda kwa wina inu zimakukhudzani chiyani?” adafunsa Abiti Patuma.

Mkulu uja adati: “Musathe mpweya, malamulo amaletsa kuchita zosayenerazi. Ngakhale malembo oyera amaneneratu.”

“Malamulowo amaneneratu kuti si bwino kugonana motsutsana ndi chilengedwe. Titati tilowe m’zipinda mwa inu mukudzitcha olungama sitikapeza mukuphwanya lamulo?” adaphaphalitsa funso Abiti Patuma.

Abale anzanga, mwinatu mukufuna kumva maganizo anga pankhaniyi. Ndine mmodzi mwa anthu amene amakhulupirira kuti ngakhale nyerere zimadziwana kuti iyi ndi yaimuna, iyo yaikazi, chimodzimodzi agalu, abakha, nguluwe ndi akamba. Chinanso nchakuti tikadati tonse tiziganiza chomwechi, bwenzi dziko ndi anthu ake alipo?

Koma mbali inayi, zochitika kuchipinda kwa ena ine sizindikhudza; ndilibe nazo ntchito. Pamene ena akuchita kusaweruzika ine sindikhala nazo ntchito.

Zonse zili apo, ndimakhulupirira kuti chilengedwe chiyenera kutsatidwa basi. Ndimaopa kuti zipata zitatsegulidwa, mwana wanga Zeno akhoza kuona ngati kukhalira limodzi atambala okhaokha palibe chachilendo.

Gwira bango! Upita ndi madzi iweeeee! n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »