Za Sipho Waola pa Wenela

Listen to this article

Sipho Waola pa Wenela

 

 

Kunali Joni, Chilembwe

M’boma la Chiradzulo

Anali mbusa

Wamphamvu

Iyitu ndiyo nyimbo imene idayala nthenje pa Wenela tsikulo. Ndithu, timalingalira kuti adapha Chilembwe kwenikweni ndani? Inde tikudziwa munthu wa Mulunguyu ankagwiritsa ntchito mfuti zimene adalanda ku Mandala pokwapulira azungu, osati kuombera chifukwa samadziwa kagwiritsidwe ntchito kake. Koma ife ndani kuti timutonze mkulu ameneyu, amene nkhope yake lerolino ili pandalama! Amene muku n y o z a Chilembwe, nkhope yanu ili pandalama? Idzakhalapo pa ndalama?

art

Musaiwaletu ku t i nthawi ina uyu Mpando Wamkulu adali pandalama, ena adamuchotsapo. Lero akungoyenda zyolizyoli ngati akutola singano!

Kodi mumayesa kukhala pandalama ndi masewera? Mfumu Mose ili pandalama? Nanga Adona Hilida ali pakhobidi? Za Moya Pete musachite kunena! Angaoneke nkhope yake pandalama munthu wofuna kusakaza mamiliyoni kuti agule chimbudzi choyenda nacho, kungomva kuti ano ndi masiku a mobile phones?

Sindidziwa kuti nyimbo, kapena nthabwala ya Madolo, inde Kennedy Ndoya, idabwera bwanji. Adaika ndi Gervazzio.

Khirisimasi ndi Januwale, uhmm!

Zalowa m’manyumba (sic)

Zaseseratu

Inde, amene amakwera basi ayamba kuyenda pansi….

Koma kodi dolo ameneyu adangosowa bwanji?

Ndikumbuka tsiku lina atafika kwathu kwa Kanduku. Adati: “Onse a ku Ntcheu ndinu madolo, imikani manja ndikuoneni!”

Atangotero, onse a ku Ntcheu adaimika manja.

“ Imi r i r a n i an thu akuoneni,” adapitiriza.

Namtindi wa anthu a ku Ntcheu udaima.

“Ndinu zitsiru anthu a ku Ntcheu. Zoona mungamapite kumudzi kukanena kuti ndikuvutika? Ndinu zitsiru anthu a ku Ntcheu!” adatero.

Mas iku amenewo, asanatseke PTC ya pa Mphate. Inde pa Mphate pa Eneya!

Tsonotu nkhani il i mkamwamkamwa ndi ya uyu mbale wathu amakonda kuika phazi lake mkamwa: Gerie Waola. Panotu tikumva kuti mkulu adanyachula ndi nkhani ya ndege ya Moya Pete uja tsopano wapezeka ndi zithunzi za kamsungwana aka Sipho Kayale!

Koma abale!

“Mkuluyu ali ndi miyoyo yoposa ya mphaka. Ngakhale anzake amene adadya nawo mbale imodzi, ngakhalenso kucheza ndi mkazi mmodzi alephera kumusuntha,” adatero Abiti Patuma.

Tonse tidangoti chete, kusowa chonena. Nanga tikadatipo chiyani?

“Ndidadziwana naye kale nthawi imeneyo akufuna mpando wa ukhansala kuchigwa cha Shire. Nthawiyo ndinkamuvinitsa ku Nandolo ku Chilomoni. Sadasinthe chifukwa nthawi zonse amafuna kupanga udani basi,” adatero iye.

Abale anzanga, palibe icho ndimatolapo

Gwira bango Gerrrrriiiiiee! Upita ndi madzi. Anzako akudya nawo limodzi asangalale! n

 

Related Articles

Back to top button