Chichewa

Za ukamberembere mu Fisp akuti zichepe chaka chino

Listen to this article

 

Ntchito yotumiza zipangizo zaulimi zotsika mtengo mupologalamu ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) ili mkati koma nyengo ngati iyi atambwali ofuna kulemera m’njira zachinyengo amachuluka.

Atambwali oterewa akuti amalowerera msika wa zipangizozi ndi njira zosiyanasiyana ndipo pamapeto pake zipangizozi zimakathera m’manja mwa anthu ochita bwino kale mmalo mwa anthu ovutika omwe ndi eni pologalamuyi.

Apolisi, unduna wa malimidwe ndi bungwe la mgwirizano wa alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) ati chaka chino salekerera zachinye za mtundu uliwonse mupologalamuyi kuti anthu oyenerera okha ndiwo apindule.

Alimi ena m’chigawo cha kumwera monga awa ayamba kale kugula zipangizo zotsika mtengo
Alimi ena m’chigawo cha kumwera monga awa ayamba kale kugula zipangizo zotsika mtengo

“Kumbali yathu, tilimbikitsa chitetezo potumiza apolisi ambiri m’madera ndi m’misika yomwe pologalamuyi ikuchitikira. Tigwira ntchitoyi kudzera mu nthambi yathu ya chitetezo cha m’mudzi ndipo ndikunena pano takonzeka kale,” adatero wachiwiri kwa wamkulu wa polisi m’dziko muno Rodney Jose.

Iye adati mmene pologalamuyi imayamba, boma lidapereka mphamvu zoyang’anira chitetezo cha zipangizo zotsika mtengozi m’manja mwa apolisi ndipo amaigwira mogwirizana ndi unduna wa zamalimidwe ndi bungwe la alimi la FUM.

“Chiyambireni pologalamu iyi, tagwirapo akamberembere ambiri. Milandu yambiri imakhala yokhudzana ndi anthu kupezeka ndi makuponi achinyengo, ziphuphu ndi kuzembetsa zipangizozi ndi cholinga chokagulitsa kumaiko akunja,” adatero Jose.

Mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe Erica Maganga adati ndi udindo wa mafumu ndi anthu awo kutsina khutu akuluakulu akaona mchitidwe wokayikitsa pakagawidwe, kagulitsidwe ndi kapezedwe ka zipangizozi.

Maganga adati boma limaononga ndalama zambiri mupologalamu ya sabuside n’cholinga chotukula alimi ovutika ndipo ngati zipangizozi sizikuwafikira ndiye kuti zolinga za boma sizikukwaniritsidwa.

“Anthu ndiwo amaona zomwe zimachitika m’madera mwawo ndiye iwo ndi amene angakhale oyambirira kukanena kuti akamberemberewo agwidwe ndipo zipangizo zawo zaulimi zipulumuke,” adatero Maganga.

Wapampando wa bungwe la FUM Prince Kapondamgaga adati chitetezo chitakhwima, pologalamu ya sabuside ikhoza kusintha miyoyo ya alimi ang’onoang’ono omwe sangakwanitse kugula zipangizo za ulimi paokha.n

 

 

Related Articles

Back to top button
Translate »